A NDUNA A ZACHUMA ALIMBIKITSA A MALAWI PANKHANI YAKUGWA KWA KWACHA

M’mawawu kunali mkumano wa Nduna ya Zachuma ndi atolankhani ku BICC mu nzinda wa Lilongwe.

Kunali chitetezo chokhwima ku maloku kumene nduna yazachuma a Simplex Chithyola Banda amachititsa msonkhano wa atolankhani.

Pamsonkhanowu a Chithyola Banda amafotokoza ndondomeko zomwe boma layika pofuna kuchepetsa ululu umene a Malawi angakumane nawo potsatira kutsika mphamvu kwa ndalama yakwacha ndi K44 pa K100 iliyonse.

Mkati mwa chipinda cha msonkhanowu munali achitetezo ochuluka.

Komabe atamaliza kuwerenga lipoti la ndondomekozi a ndunawa sanayankhenso mafunso kwa atolankhani.

ZINA ZIMENE A NDUNA ANALANKHULA NDI IZI

A ndunawa alengeza ndondomeko zili m’mumsizi, zimene boma lakhazikitsa potsatira kugwa kwa ndalama ya Kwacha:

  1. A Malawi okwana 184,920 amene anakhudzidwa ndi Cyclone Freddy adzilandira K50,000 pamwezi kwa miyezi itatu.
  2. Mabanja okwana 105,000 okhala mtauni azilandira K150,000.
  3. Boma litumiza achinyamata okwana 5000 kukagwira ntchito ku mayiko akunja
  4. Anthu pafupifupi 2,741 akhala akulembedwa kukagwira ntchito mu unduna wa za umoyo.
  5. Boma lili kaliki liki likukambirana ndi olemba ntchito kuti akweze malipiro a anthu ogwira ntchito.
  6. Boma laletsa kugulitsa ndalama pa msika osavomerezeka (black market).

Ndunayi yatinso boma lakhazikitsa ndondomeko zomwe zithandizire kubwezeretsa chuma cha dziko lino m’chimake. Ndondomeko zake zili motere;

  1. Boma liyamba kugulitsa mpweya (carbon credit) m’mayiko akunja.
  2. Boma likufuna lipeze kuchuluka kwa miyala ya mtengo yapatali yomwe ilipo mdziko muno kuti liyambe kugulitsa m’mayiko akunja.

3.Boma likufuna lipeze misika ya chamba m’mayiko akunja

Malinga ndi undunawu, atsimikiza kuti ali ndi chiyembekezo choti boma likhoza kupeza ndalama zosachepera $5 Million mu zaka ziwiri zikubwerazi.

Zambiri tsatani Avantmalawi.com

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *