Ntchito yokonzekera kumangaso Mlatho watsopano wa Lilongwe udakali mkati, ndipo tikunena pano Ntchitoyi wasongola pamene tsopano milatho iwiri itsegulidwe.
Kutengera ndi olankhulira kampani ya Boma pazomangamanga komanso miseu (Roads Authority) watsimikiza kuti Milatho iwiri tsopano yogwirizirayi iyambe kugwira ntchito pa 16 November ndipo mlatho wakale uzatsekedwa.
Milathoyi ayitsegulira pakukonzekera ntchito yomwe ikuyembekezereka kugwiridwa pomangaso Mlatho wa ukulu umene umalumikiza Msika wa Area 2 mu tawuni ya Lilongwe ndi Nseu odutsa area 3 police kupita ku Likuni komanso madera ena monga area 18, 25 komanso 49.
Milatho iwiri yamangidwayi izigwiritsidwa ntchito zosiyana, pamene kwakonzedwa kwina kodutsa anthu oyenda pansi komanso pamene mbali ina kuzidutsa magalimoto.
A Kondwani Munthali amene ali othandizira kuyang’anira milathuyi atsimikiza kuti ntchitoyi yatsala pang’ono kutha. Komanso awunikira kuti mlatho watsopanowu ukhala ndi misewu isanu komanso ina yapadera yoyenda anthu oyenda pansi.
Ntchito yonse ikuyembekeza kutha chaka cha 2026 ndipo izafunikira ndalama zokwana k24 million zimene akuthandiza ndi ndi boma la Japan.
Avant Publications