UTHENGA WA CHISONI KUBANJA LA A KATENGEZA

Malingana ndi a Hexin Katengeza, omwe ndi mlongo wawo wa oyimba otchuka ndi Nyimbo za Uzimu a Estiner Katengeza atsimikiza za imfa ya mchemwali wawo a Agnes Katengeza amene apezeka ataphedwa ku Lilongwe.

A Agnes Katengeza adasowa dzulo ndipo lero apezeka ataphedwa mu galimoto lawo number plate BY5149 ku Lilongwe. Zatsimikizika kuti a Katengeza omweso amachita business ya zodzola dzola mu nzinda wa Lilongwe amwalira.

“Thupi la a Katengeza linapezeka ndi mabala omwe titha kutsimikiza kuti achita kuphedwa koma zitengera a polisi kutsimikiza za Nkhaniyi.” Atero a Hexin, mlongo wawo wa Katengeza.

Kuphedwa kwa a Katengeza kukudza patangotha masiku pamene mzibambo wina Allan witika ogwira ku Carsbeg anapezekaso ataphedwa ku Lilongwe komweko.

Kufikira pamene timalemba nkhaniyi, a polisi anali asanalankhulepo za nkhaniyi kapena kutsimikizira a Malawi za chitetezo chawo dziko muno.

Zambiri tsatani avantmalawi.com

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *