APHUNZITSI AWIRI AMANGIDWA KAMBA KOFUNA KUBERA MAYESO

Pamene ophunzira a folomu 4 ali mkati molemba mayeso a MANEB apolisi mu nzinda wa Blantyre amanga mphunzitsi wa pa sukulu ya sekondale ya Finnish Line Private ku Machinjiri mu nzinda wu a Gift Maguza powaganizira kuti anajambura ndi lamya yawo ya m’manja malangizo a chinsinsi a mayeso a phunziro la Agriculture Practical ndi kutumiza kwa mphunzitsi wina wa pa sukulu pomwepo.

Mโ€™neneri wa bungwe la MANEB a Mayamiko Chiwaya watsikiza za nkhaniyi ponena kuti mโ€™boma la Chiradzulu, a polisi a ku sakasakanso a phunzitsi ena awiri a pa sukulu ya sekondale ya St. Joseph Catholic Private powaganizira kuti achita chimodzimodzi la chitatu pa phunziro la Biology.

A Chiwaya ati bungwe lawo ndi lokhumudwa kuti za chinyengozi zachitidwa ndi a phunzitsi omwe amayenela kulimbikitsa ophunzira kulimbikila kuwelenga komanso kupewa za chinyengo pa mayeso.

Pakadali pano wachiwiri kwa mโ€™neneri wa nthambi ya polisi m’dziko muno a Harry Namwaza wachenjeza kuti a polisi amanga aliyense yemwe atapezeke akuchita za chiyengo pa mayesowa .

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *