MASAMBA A MCHEZO AKULOWETSA PANSI MAPHUNZIRO

Katswiri pa nkhani za maphunziro a Benedicto Kondowe ati aphunzitsi asiye m’chitidwe okhala pa masamba a mchezo pa nthawi yomwe akuyenera kuphunzitsa kamba koti m’chitidwewu ukupititsa maphunziro pansi.

Katswiriyu wanena izi kutsatira dandaulo la anthu okhala m’boma la Mangochi pa mwambo owunikira mnene bomali likuchitira pa nkhani za umoyo, ulimi ndi maphunziro.

A Kondowe ati chomwe aphunzitsi akuyenera kudziwa ndi choti nthawi yambiri yomwe amakhala pa masamba a mchezo monga WhatsApp, Facebook amakhala kuti akuwononga nthawi yomwe akanaphunzitsa Ana sukulu.

Pakadali Pano katswiriyu wapempha a phunzitsi akulu m’masukulu kuti aziyendera aphunzitsi m’makalasi pa nthawi yomwe akuphunzitsa kuti m’chitidwewu uchepe,komanso aphunzitsi kumagwiritsa ntchito lamya pokhapokha zili zogwirizana ndi maphunziro pa nthawi yomwe ali mmakalasi.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *