A POLISI KU LILONGWE ALANDA GALIMOTO 46 PA MILANDU YOSIYANA SIYANA

A polisi ku Lilongwe lero alanda galimoto pafupifupi 46 pa milandu yosiyana siyana kuphatikizapo kunyamula matola ndi kusakhala ndi zikalata zoyenera.

Malingana ndi mneneli wa polisi ya Lilongwe a Hastings Chigalu ati ntchitoyi yomwe idayambika mwezi wathawu yakwanitsa kulanda galimoto zokwana 126 tsopano.

Iwo ati galimoto zina zimanyamula matola pomwe nzosalembetsedwa kuti zichita izi.

Iwo ati galimoto zina zalandidwa kaamba koti omwe amayendetsa galimotozo analibe zikalata zowavomereza kuyendetsa galimoto.

Iwo awonjezera kuti izi zikuchitika m’mizinda yonse ya mdziko muno molingana ndi malamulo a pa msewu ndi cholinga chofuna kubweretsa bata pa msewu.

Iwo alangiza omwe akufuna kumachita matola ndi galimoto zawo kuti aziyamba alembetsa kaye asanaymbe kuchita izi.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *