“TELEMU INO MUSAPITESO KU SUKULU” –

watero unduna waza maphuziroUnduna waza maphuziro wati ophuzira a sukulu zapulaimale komaso sekondale maboma ena khumi chigawo chakum’mwera ndi kum’mawa omwe akhudzidwa ndi Namondwe wa Freddy angomaliza telemu ino ali pakhomo asapiteso ku sukulu.

Sabata yatha unduna-wu unalengeza kuti ophuzira a m’maboma khumi (10) monga Blantyre, Zomba, Chiradzulu, Nsanje, Thyolo, Mulanje, Phalombe, Chikwawa, Mwanza komaso Neno asapite ku sukulu akhale pakhomo kaamba ka chiopsezo chomwe Namondwe wa Freddy amapeleka m’maboma-wa. Unduna-wu ukuti wapanga izi utalandira upangiri wapadera kwa a katswiri aza maphuziro ndipo izi zikutanthauza kuti ophuzirawa adzayambaso maphuziro awo pa 17 April, chaka chino.

Kudzera mu chikalata chomwe unduna-wu watulutsa ndipo wasainira ndi mlembi wa mkulu mu unduna-wu Chikondano Mussa chikunenaso kuti ophuzira onse omwe ali pafupi kulemba mayeso akayambaso sukulu pa 27 March ndipo ena onse omwe amayenera kulemba mayeso telemu ino adzalemba mayeso-wa akakayambaso sukulu.

Avantmalawi.com

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *