ANTHU SANAGONE KU FATIMA, NSANJE

Ma report amene avant akutipeza zikuonetsa kutu anthu amene Ali mu ma camp oposera khumi ku Nsanje, Fatima ndi Makhanga usiku wapitawu sanagone tulo.

Izi zachitika pomwe kagulu kena ka anthu kananamiza anthuwa kuti kudutsa chivomerezi komanso madzi osefukira.

Anthuwa akhala Ali Tcheru usiku onse kudikira chivomerezi chimenechi ndipo kufikira padakali pano sichinadutsebe.

Polemba pa Tsamba la Mchezo mphungu wa delari wadandaulira anthu kuti asamanamizane ndipo azidikira uthenga ochokera kwa za a nyengo.

NSEWU WOPITA KU FATIMA KUDZERA KU THYOLO WADUKA

“Ndi zithu zokhumudwitsa kuti ena anapanga chisankho chonamiza anzawo mu mtundu otere. Kunoko anthu oposera 2,000 akukhala mma camp opeseraso 10 ndipo akusowekera thandizo la zakudya ndi zofunda. Ndiye tikuyesa yesa kuwapezera zakudya, wina mkumawanamizaso sizinthu zabwino. Komabe Tithokoze boma potitumizira matumba a chimanga lero kudzera pa ndege za khondo.” Chizuzu, mpungu wa Nsanje North.

Nsanje north, kumapezeka madera monga fatima, masenjere, Makhanga ndi ena ndipo padakali pano misewu yonse yopita kumaderawa kuchoka ku Nsanje boma kapena ku Blantyre yaduka.

Zambiri tsatani avantmalawi.com

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *