MARTHA CHIZUMA AMUTSEKULIRA MLANDU

Mkulu wa bungwe lothana ndi katangale ndi ziphuphu la ACB, Martha Chizuma amusumilanso ku bwalo la milandu pomwe tsopano mbali ya boma ikuti mayiwa adanena oweruza wa ku bwalo lalikulu la milandu Simeon Mdeza kuti ndiwakatangale.

Izi zikuchokera pa mau otepedwa omwe anafala pa masamba a mchezo chaka changothachi pomwe a Chizuma amayankhulana ndi munthu wina nkhani zokhudza ofesi yawo.

Kalata ya mulandu yomwe taona yati a Chizuma akuyenera kukaonekera ku bwalo lamilandu lero, kukavomera, kapena kukana mlandu wa tsopanowu.

Izitu zikudza patangotha sabata zingapo mbali ya boma itanena kuti yathetsa mulandu wina omwe mkulu wakale ozenga anthu milandu, Dr. Steven Kayuni anatsegulira a Chizuma pa mawu otepedwa omwewa.

Pakadali pano oyimira a Chizuma pa milandu, Martha Kaukonde sadayankhulepo pa nkhaniyi.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *