Chirombo cholusa chavulaza anthu M’boma la Dedza

Kunali chipwirikiti M’boma la Dedza pa 19 January 2023, pamene ma lipoti akutsimikiza kuti anthu ambiri avulazidwa ndi Chirombo chokhala ngati Fisi.

Chirombochi chinatuluka kumanda m’mudzi mwa Dambe, kwa Mfumu Yaikulu Chilikumwendo.

Pamene Nthawi inali 4 koloko ku m’mawa, chirombochi chinagwira Munthu ochita bizimisi. Munthuyu anachitika mwayi kuti pa nthawi imene amakuwa anthu omwe anali pafupi anamupulumutsa, koma Chirombochi chinayambaso kuluma anthuwo.

Ma lipoti osatsimikizika ndi apolisi akusonyeza anthu asanu ndi anayi avulala kwambiri kuphatikizapo mzimayi amene chachotsa nkhope yake molapitsa.

Chirombochi chaphedwa ndi a polisi a pa Kabwazi.

Amene tikukumbikira Chirombo ngati chomwechi chinavutaso mu chaka cha 2005 m’mudzi mwa Chiombola m’boma la Dedza lomweli ndipo anthu ochuluka anaphedwa.

Tsatani zambiri pa
avantmalawi.com

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *