Timu ya Nyasa Big Bullets Reserve yakwanitsa kuteteza ukatswiri wake wa chikho cha K8.3 Million Nyasa Capital Finance chomwe anatengaso chaka chatha mu muchigawo chakumwera, pomwe lero yagonjetsa timu ya Ndirande Stars 2-1 pabwalo lazamasewero la Kamuzu Stadium.
Masewero anali apamwamba mbali zonse, koma inali Bullets Reserve pa mpindi ya 58 yomwe inayamba kugoletsa kudzera mwa Emmanuel Saviel , kenako pa mphindi ya 80 Chikumbutso Salima anayika chigoli chachiwiri cha Reserve pofuna kuyisefa Ndirande Stars.
Masewero akupita kumapeto anyamata ochaka mu mdera la Ndirande anapeza chigoli chawo chopukutira misozi anthu amusika wa. Ndirande omwe amayembekezera kuti mwina chikhochi chifika kwawuku lero.
Kutsatira ukatswiriwu, Bullets Reserve yalandira K1.5 Million pomwe Ndirande yatenga K600,000.
Pamasewero opeza timu yanambala yachitatu, Balaka FC inagonjetsa timu ya Nsanje United 3-2 mumapenate , Masewerowa 90 atathera 2-2.
Balaka pomaliza panambala 3 , ilandira K250,000 pomwe K100,000 iperekedwa ku Nsanje United.Mphoto yakatswiri omwetsa zigoli zochuluka yapita kwa Gift Lamowa wa Ndirande Stars yemwe wamaliza ndi zigoli, 9.