Kumayambirilo a sabata ino mfumu ya mzinda wa mzuzu a Gift Nyirenda anamangidwa kamba koti anagwilirira mwana.koma tikunena pano bwalo la milandu ku mzuzu lapereka belo kwa khansalayu.
Nkhaniyi yachititsa chidwi amalawi ambiri kamba koti nthawi zonse anthu ogwilirira mwana matsiku ano samapatsidwa belo ndipo zaka zake zinaonjezereka kamba koti mchitidwewu umakula kwambiri.
Lero angakhale mwanayo anakachita kusuma yekha kupolisi bwalo lamilandu lati aliyense alindi ufulu otuluka pa belo. Ndipo a Nyirenda simunthu oti angathawe poti ndi oziwika. Nkhaniyi kunena zoona sinayende pachilungamo kamba koti onse oganizilidwa kugwilira ana samapatsidwa belo masiku ano.
Masiku apitawa taona ma jaji akudzudzulidwa kwambiri za mchitidwe osagamula bwino milandu. Nkhaniyinso ndi imodzi mwa nkhani zomwe ma jaji amayenera kukonza, kodi tidziti awa apatsidwa belo poti ndi khansala? Kapena poti ndi mayor? Kapena mwina poti ndi wachipani cholamula?
Nkhani zambiri zikapita ku khoti ndipo munthu akapatsidwa belo timadziwa kuti nkhaniyo yatha, ndipo singalowenso msanga mubwalo. Kunena zoona ndende zikudzadza ndi amphawi. Avant publications insatiable mwachidwi nkhaniyi.
www.avantmalawi.com
DR MWALE