RAS CHIKOMENI AZAIMANSO 2025

Mu chaka cha 2020 Ras chikomeni chiwa anakodola chikoka cha ma rasta onse mmalawi muno komanaso achinyamata ambiri omwe anakamuperekeza ku comesa hall ku Blantyre komwe amakasiya zikalata zake ku bungwe loyendetsa chisankho.

Chikomeni chirwa analephera kuimira kamba koti sanakwaniritse kupereka ndalama yokwana 2 million kwacha yomwe imafunika munthu ukafuna kuimira pa mpando wa president.

Nkhani ya chikomeni chirwa inautsa mpungwepungwe ponena kuti ndalama yomwe anthu amapereka ndiyochukuka kwambiri. Koma bungwe la MEC limachita izi ponena kuti amafuna anthu okhaokhawo omwe ali siliyasi osati kungoyesa ayi, mwachitsanzo kunena kuti ndalamayi ikhale yochepetsetsa aliyense atha kumafuna ataimila zomwe zizakhale zongochulutsa ntchito.

Koma mmawu ake Ras chikomeni chirwa ati iwo akadali ndi chidwi chofuna kuzaimira pa mpandowu ndicholinga chofuna kuzasintha zinthu mdziko muno. Ndipo iwo akudziwatsa amalawi onse za khumbo lawoli ndipo apempha amalawi akufuna kwambwino kuti azawagwire zanja pa nthawiyo kuti khumbo lawo likwanilitsidwe

A Ras chikomeni chirwa anatenga mayi awo omwe anali wachiwiri wawo pa chisankho cha 2019 ndipo sizikuziwika ngati azachitenso chimodzimodzi

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *