A BUSHIRI AKONDEREDWA NDI BWALO LA MILANDU

THE MATTERIS IN COURT

Bwalo la milandu ku Lilongwe lakana pempho la boma kuti mboni za ku South Africa zipereke umboni ku ma bwalo a dzikolo.

Zomwe boma limafuna ndi zakuti mboni zaku South Africa zipite mu khoti kukayamba kupereka umboni omwe uzikajambulidwa ndipo akamaliza bwalo laku South Africa lizatumiza zojambulazo ku malawi kuno kuti zizagwire ntchito mu khoti. Koma oyimira bushiri ati mbonizi zibwere kuno azazifunse mafunso okha.

A chimwaza apereka chigamulo ponena kuti mbonizo zikufunika kuti zibwere kuno kuzapereka umboni, komaa oyimira boma pa milandu auza bwalo kuti kubweretsa mbonizi kuno kutha kuononga ndalama zambiri. Koma lawyer wa a bushiri a wapona kita ati izi sizoona.

Pakadali pano oweruza mulanduwu wati mbali zonse zibweretsenso mfundo zawo mmatsiku 14 kuti azaunikenso mulanduwu ndikupereka chitsogozo popeza kuti aka ndikoyamba mulanduwu kuchitika

A bushiri akufunika ku South Africa pa mulandu ozembayitsa ndalama.

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *