Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos chilima ayankhula ku mtundu wa amalawi zomwe zakhala zikuchitika mziko muno.
Malingana ndi chiyembekezo cha amalawi ambiri amayembekezera kuti chilima ayankhula zambiri zokhuza katangale komanso kutchulidwa kwawo mu lipoti la bungwe la ACB. komatu izi sizinali choncho kamba koti achilima sanachedwepo pa nkhani ya katangaleyi.
*ati chani pa nkhani ya katangale?*
Achilima ati akudziwa za nkhani ya katangale yomwe ili mdziko muno komanso za kutchulidwa kwawo ndi ACB. Poyamba iwo awuza amalawi kuti ndiwo omwe anayamba kukamba nkhaniyi mu nthawi ya kampeni kuti president asamakhale otetezedwa kuti asamafufuzidwe akapalamula mulandu kapena akachita zachinyengo nthawi yomwe ali pa mpando. Nkhaniyi ili pa section 91 mu malamulo akulu adziko lino. Mawuwa sikuti angotchulidwa koma kuseri kwakeko kuli zambiri zomwe anthu ambiri sakumvetsa. Nditambasule motere. Chilima wavomereza kuti ngati iye anatchulidwa mu lipoti la ACB ndekuti akudikira bungweri kumutengera ku khoti ndipo iye ali okonzeka kukayankha zomwe akudziwa pankhayi koma poti pakadali pano sakuziwa zomwe iye anachita naye sangayankhepo poti ACB sinafotokoze chomwe anachita. Iwo awuza osatira chipani chawo kuti asaletse ACB kuti kuti izawafunse mafunso. Komanso ponena zoti president azifufuzidwa iye waona kuti mtsogoleri wa dziko lino naye ndi okhuzidwa pa nkhani za katangale ndipo sakutchulidwa poti malamulo amamuteteza kusiyana ndi wachiwiri wake. Apa chilima akumbutsa amalawi kuti imodzi mwa mfundo ya mu mgwilizana ndi yoti azasinthe lamulo 91 la mu malawmulo akaye ndetsedwe ka dziko. Zomwe zikangosinthidwa chakwera atha kufufuzidwa. Koma mpaka lero bilu imeneyi sikupita ku Parliament. Chilima sanakane kapena kuvomera kuti anachita za katangale kapena ayi koma wati ACB ichite changu kuti iye amutengere ku khoti akayankhe.
Dzina zomwe amakamba ndi momwe iye amagwilira nthito ndipo apa sitichedwapo. Koma achilima apezerapo mwayi kuuza amalawi zomwe zili mu mgwilizano.
*Walankhula zotani za mgwilizano*
Achilima ayamba ndi mawu omwe ananena sabata yatha kuti kuzichepetsa kwawo kusaoneke ngati kupusa. Iwo awuza mtundu wa amalwi kuti pomwe amapanga mgwilizano mu March 2020 omwe unakasainidwa pa 19 March sikuti unangochitika koma panali anthu omwe anayendetsa izi. Ndipo anthuwa ndi a mpingo ndi ma loya, komanso otsatira zipanizi omwe anatumidwa kugwira ntchitiyi. Iwo atchulapo a Dr silungwe, a kapondamgaga ndi ena kuti anali nawo popanga mfundo za mgwilizano. Achilima ati zipani zonse ziwiri zimakhala pansi kupanga mfundo za mgwilizano zomwe atamaliza anasainilana kuti zisazaphwanyidwe. Mfundo yaikulu kwambiri inali yoti wina akakhala president 2020 ndekuti wina akhala vice koma yemwe ali president ulendo uno sazaimiranso chaka cha 2025. Koma wachiwiri wake ndi yemwe azaimire. Ndipo zipani zonse zizapatsana support. Achilima ati mbali zonse ziwiri zinagwilizana kuti pasapezeke chipani chopambana mphamvu kuposa chinzake, maudindo agawane mofanana, komanso pasapezeke aliyense ophwanya mgwilizano chifukwa izi zinasainidwa ndi azamalamulo. Mumvetsetse apa malamulo awa ndi a mugwilizano wawo osati a dziko.choncho kuphwanyidwa atha kusumirana.
Achilima ati ndiodabwa ndi zomwe zayamba kuchitika poti pena mfundo za mgwilizano zayamba kuphwanyidwa popanga ziganizo. Nkhayi yabwera pomwe a chakwera anawaimitsa a chilima asanakambirane za lipoti la ACB.
*Mgwilizano unali wa nthawi yotalika bwanji?*
Achilima ati mgwilizanowu ndi wa zaka 10 ndipo zaka zisanu alamula ndi chakwera kwinako azalamule ndi iyeyo. Nde palibe chifukwa choti UTM ichokere mungwilizano. Apa ndipomwe panabwera miyambi yoti bwato satsitsirana panjira, komanso omwa msuzi sasamba mmanja nsima isanathe, kuthandauza kuti UTM ndi yomaliza kulamula choncho singatuluke mu mgwilizano mpaka utafika kumapeto.
Komabe achilima ati ngati MCP ikufuna utm ituluke mu mgwilizano aneneretu kuti aliyense ayende yekhayekha koma aziwe kuti boma ili ndi losokherana nde apite kumasankho iwo azawine pawokha, ngati akane kupita kumasankho mgwilizano sungathe popeza anasokha nawo.
Izi ndi zomwe wayankhula mtsogoleri wa dziko lino.
www.avantmalawi.com
*DR MWALE*