KULUMIKIZA MADZI KWA ULELE KWATHEKA

Boma kudzera mu unduna owona za madzi ndi ukhondo sopano walengeza kuti bungwe logawa madzi la waterboard  liyamba kulumikiza madzi mwa ulele kuyambira la chisanu pa 1 April 2022.

Nkhaniyi yadza pomwe mtsogoleri wa dziko lino a Chakwera alamula kuti ntchitoyi yomwe inali imodzi mwamalonjezano awo mu nthawi ya kampeni tsopano iyambike.

Kuyambira kale bungwe lolumikiza madzi limauza anthu omwe akufuna madzi kuti apereke ndalama yolumikizira madziwo pambali poti agula kale zipangizo okha, akatero amayera kudikiranso chinthawi kuti ntchitoyi ikatheke. Malingana ndi Boma izi zimapangitsa kuti anthu osowa asamakhale ndi madzi a ukhondo mmakomo mwawo ndipo zimabweretsa matenda osiyanasiyana kamba komwa madzi osatetezeka, chatero chikalata cha bomachi.

Nduna yooona za madzi ndi ukhondo olemekezeka a Abida Mia omwenso asainira chikalatachi ati boma likufuna kukwanilitsa mfundo zomwe dziko lino likutsata kuti pofika 2063 malawi akhale otukuka, komanso kuti mfundo za bungwe la United Nation lofuna lukhala ndi madzi a ukhondo kwa aliyense pofika 2030 likwanilitsidwe.

A Mia ati boma laika ndondomeko ya kagwilidwe ka nchitoyi komwe kafotokozedwe bwino lomwe lachiwiri sabata ya mawa  pa msonkhano wa atola nkhani kuti amalawi amvetse bwino komanso kuti bungwe la waterboard  litsatire pogawa madzi kwa amalawi.

Pa ulendo omwe president ndi wachiwiri wake anali kumwera wachiwiri kwa president analankhula ku thyolo kuti poyamba kunali covid 19 yemwe anatifinya koma pano wachepekapo ndipo tikudziwa kuti zinthu sizili bwino ndiye pano  zambiri zomwe tinalonjeza ziyamba kuchitika amalawi tisataye mtima.

www.avantmalawi.com

*DR MWALE*

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *