CHENI CHENI NDI CHITI A MLAKA MALIRO?

Sabata lapitali Oyimba otchuka amenenso ali m’busa a Mlaka Maliro analembera Kalata Mtumiki wa Enlightened Christian Gathering (ECG) kumupempha kuti afuna atule pansi udindo ngati M’busa wa Mpingowu ku Eswathini.

Muchikalata chimene a Mlaka Maliro analemba, anafotokoza kuti iwo aganiza zimenezi pofuna kukhala ndi nthawi yambiri ndi Banja lawo komanso mayitanidwe awo a zamayimbidwe.

Atafunsidwa a Mlaka Maliro, anati iwo sakusiya Ubusa pakuti awa ndi maitanidwe koma akusiya kutumikira mpingo wa ECG.

Chikalatachi atachilandira a Bushiri anavomereza maganizo a m’busayu ndikuwalola kuchita zimene akufuna, a Bushiri anayamikira mlaka maliro poyimba Nyimbo yotchedwa Vinyo watha yomwe ikukamba zambiri za utsogoleri wina umene unalonjeza zithu zochuluka koma osakwanilitsa. Ambiri amene amvera Nyimboyi atsimikiza kuti a Mlaka Maliro akukamba za utsogoleri wa Tonse Alliance.

Mpingo wa ECG nawo wabwera poyera ponena kuti anthu akuyenera kuziwa chilungamo osati kukhulupirira zonse zomwe anthu akufalitsa mmasamba a mchezo. Iwo ati mpingowu unaitanitsa mkazi wa m’busa wawo mlaka malilo ku mkumano wosungitsa Bata, ndipo mpingowu sunatchule kuti mkazi wa mlaka anapalamula chani, koma mpheketsera ikumveka kuti anaitanidwa kamba ka zomwe zakhala zikumveka kuti mkaziyu akuchita chibwezi Ndi mkulu wina mu mpingomo ku Eswathini komweko, zomwe zinapangitsa mkaziyo kuthawa ku Eswati kamba koti mwini mwamunayo anaopsyeza kumuchita chipongwe ,nkhaniyi inapangitsa mlaka kuti akhale yekha ku Eswathini pomwe mkazi wake anali kuno. Aka sikoyamba kuti mkazi wa mlaka achite khalidwe ili kamba koti kumalawi kuno anamvekanso ndi mbiri zomwezi ndi mkulu wina wa bizinesi kumalawi kuno

anthu ambiri akukayikira kuti a Mlaka maliro asiya mpingo wa ECG kamba ka manyazi ndi nkhaniyi.

Mlaka maliro ndi oyimba oziwika bwino pa Malawi pano ndipo kubwerera kumaimbidwe sizingakhale zachilendo ayi ndipo a Malawi ambiri akondwera kuti zitero koma pali mpheketsera yaikulu kuti mkuluyi akufuna kuyambitsa mpingo wake.

A Mlaka Maliro anabadwa mu Chaka cha 1975 pa 3 July ndipo munthawi yawo anatulutsa zimbale monga; Dzanja lalemba, Maloto, Nkhondo, Musalire, Gologolo pa Mtengo, Njododa, Malodza komanso Pamudzi pano. A Mlaka Maliro akhala akutulutsa chimbale chomwe mutu wake akuti Vinyo masiku akubwerawa

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *