Gulu lotchedwa spiritual watchmen kumalawi lomwe lakhazikitsidwa ndi a Prophet Jonazi a mpingo wa God of Wonders ministry ku chilinde akonza mapemphero pa 12 February ku botani Garden ku Lilongwe.
A prophet jonazi polankhula ndi Avant publications ati gululi si mpingo ayi koma kuti anthu a mpingo, komanso zipembezo zonse zibwere malo amodzi ndikupemphera. Mapepherowa sasankha munthu ayi, azibusa, ansembe, atumiki, ma prophets komanso aliyense amene akutamanda dzina la yehova ndi ololedwa kubwera.
Mapempherowa cholinga chake ndi kumulilira mulungu komanso kumudabdaulira kuti chonde asatilange amalawi ndi ng’amba ndipo nyengo imeneyi iyime. Iwo akhazikika pa mawu ochokera mu yesaya, 62: 4-7. Yesterday 59: 16 komanso Daniel 4:17.
Mapempherowa akayamba 9 koloko mmawa wa lero pa 12 February ndipo kukakhala kupembezera ndi kusala kudya. anthu akuyeneraa kuvala ziguduli kwa omwe akufuna kusonyeza kudandaula kwawo.
Koma a prophet Jonathan ati ndiodzadza ndi chimwemwe kuti mawu a mu baibulo akumakwanilitsidwa nthawi zonse. Iwo ati watchers team itangolengeza za mapempherowa malemba omwe akupezeka pa yesaya 65 vs 24 akwanilitsidwa mawu akuti asanafike mawu pa lilime lanu ine ndizayankha
Usiku wathawu mvula ya mphavu yagwa mdziko muno mmadera ochuluka ndipo kwina yasasula manyumba. Koma sitilekerera ndipo mapembelowa alipobe, dzina la mulungu lipitilire kulemekezeka atero A prophet jonazi.
Avant publications.
DR MWALE
Powerful my Brother Prophet Jonaz! That’s the way to go!