OBWANDE 05 FEBRUARY 2021, BWANDE SAKUSIYA KULIZA BELU – TONSE ALLIANCE CHENJERANI

Mverani obwande mu audio ili mmwambayi

Pachichewa Pali mawu oti wamisala anaona nkhondo.mawu awa sanangobwera ayi koma anabwera ndicholinga choti zolankhula kapena maganizo a anthu ena omwe akuoneka kuti ndiopepera kwa iwo ochita bwino aziwagwilitsako ntchito.

Pali anthu ambiri omwe amati akayankhula zinthu kutsogoloko zimazachitika. Lero ndafuna ndigwilizane kwa thunthu ndi mzake wa dodolido , bwande bwantasa.

Iye mchikalata chake lero chalunjika kwa apresident a dziko lino kuti ngati sakusamala ndi maganizo a anthu ena omwe azungulidwa nawo azatha ngati a braz mmerecano.

zikuoneka ngati a cmChakwera ndi a Chilima akuiwala zomwe zimapangitsa anthu kuti awavotere. Pali nkhani zambiri zomwe amalawi zimawapweteka mmbuyomu koma anthu akayankhula palibe chimachitika.

Amalawi analonjezedwa zambiri ndi atsogoleri omwe pano ndi a Tonse alliance, kuyambira chisankho Cha 2019 komanso 2020.

Mwachisanzo.

ine ndikazatenga boma zonse zokhuza kupha ma albino ndizathesa ndipo amalawi tizadziwa yemwe amawatuma anthu amenewa awa anali mawu a president chakwera nthawi imeneyo.

Lero mwatenga boma Kodi nkhani imeneyi mwaisiya kapena tidikirebe? Mabanja a anthu omwe anachitilidwa chipongwechi zikuwapweteka mpaka lero. A Buleya Lure omwe anafera mchitokosi kamba ka nkhaniyi positidwa ndi iron yamagetsi ndi anthu omwe amayenera kuwateteza (apolisi) nkhani yawo inathera pamene paja? Lero mayi chisale omwe anavulaza Buleya lure ndi anzawo aja Kodi Basi zinathera pompaja? Zoonadi azingoyenda mwaufulu choncho? Nanga aja anaulura kuti adadi komanso a mtaba ndiwo amatenga mafupa aja nkhani yawo inatha Basi? Achakwera ndi achilima tikudikira mayankho.

Bwande waliza beru loti a dausi ndi anzawo amagula mbale ndi cup za akaidi pa K125,000 imodzi komanso ku immigration lamba bweniweni amagulidwa 75000 Kodi khani Imene ija basi munaivindikira? Nanga aja ogulitsa nkhuku 35,000 komanso chisamusa Cha 45000 aja Basi zawo zinayera?

Tinalonjezedwa ndi mtsogoleri wachiwiri wa dziko lino kuti
kumaula,ku zomba, ku mzuzu, kuchichiri kuli anthu omwe anangoba ka nkhuku, 5 years ndimaonangati amenewo achoke kuti kulowe mbava zenizeni kumeneko
Taganizano nthungululu zinaliko nthawi imene ija, Kodi zinathera kuwamanga anthu kenako atuluke pa Belo kenako ziii? Kodi mukudziwa kuti okuba nkhuku aja samapatsidwa belo?

Lero tikumva kuti 60 million ya Corona yathera ma allowance amatsiku atatu zoona? Bwande akuti akadaulo akale okuba mudakali nawo mu sisitimu yanuyo ndipo tsopano akuphunzitsani mmene muzibela ndalama Kodi kampeni ikubwerayo muzawanamiza chani amalawi pa zakatangale?

Beru likamalira ngati la bwande chonde kumalimvetsera pa mawa limazapindula.

Boma lapitalo limadana ndi Beru la obwande kamba koti limaulura zambiri ndipo kunali kukonza ma upo kuti bwande asamaveke pa wailesi . Lero beru limeneroja likulirabe kuuzanso inuyo a Tonse alliance kuti samalani amalawi sachedwa kutopaaaa, umboni wake ndi malowedwe anu a mubomaaaa.

Zoona nduna ya boma ikahale kunja kwa dziko matsiku 40? Monga boma mungatiuzeko kuti amakatani madamuwa kunjako?
Nthawi Zina mmaipatsa dala mfiti yaikazi zolankhula lero nkhani ndi yawo madamuwa deputy, mwawapatsa dala zolankhula anthu.

Inde mwalowa mmuboma nthawi ya Corona koma musaiwale kuti tinavota Corona alipo, ndipo malonjezo amabwera Corona alipo.

Ndalama zija zofuna kugawira amalawi zija Kodi zili kuti? Simukuona kuti nthawi yogawa ija ndi ino?

Nayo ngongole ya madefu kuli zii mpaka lero koma anthu munawalonjeza kupanga magulu kuti ndalama ziyambe kuperekedwa January koma lero February ndi uyu kuli ziiii.

Mkatikati mwa boma la Tonse muli njoka Zina zomwe zangobisala ndipo si zanu a Tonse alliance ngati simusamala muzagwa Cha gada 2025 kamba koti alendo omwe mukulandirawo alindi kampeni ku mphatsa koma inuyo simukuona.

Ife sitizasiya kuliza beru kuti ali ndikhutu amve.

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *