National Bank Ilonjeza kutukula ntchito za ICT

olemba Wongani Chipeta

Banki ya National (NBM) yauza anthu omwe amachita malonda ogwiritsa ntchito makina a ma kompunta komanso internet polandira, kusunga ndi kutumiza uthenga kuti alimbikitse ntchito zawo kuti zipite patsogolo. Bankiyi yauza amalondawa komanso achinyamata kuti akhale anthu oganiza kupititsa patsogolo malondawa kuti pakhale kupikisana ndi achinyamata ochokera mmayiko osiyanasiyana padziko lapansi.

Wachiwiri kwa Chief Executive wa Bankiyi a Harold Jiya walankhula izi pa msonkhano wa bungwe la anthu opanga bizinesi za ICT la ICT Association of Malawi(ICTAM) womwe unachitikira ku Mangochi lachisanu lapitali.

A Jiya anati Banki ya National ndiyokonzeka kupereka ndalama zothandizira achinyamata aza ICT kukwaniritsa maloto awo opanga chuma pogwiritsa ntchito luso la za makomputa ndi technology.

Iwo anati National Bank ya Malawi imamvetsetsa komanso imathokoza pa zomwe gawo la luso ndi ukadaulo wa ntchito za ICT limapanga potukula chitukuko cha dziko lino la Malawi.

Zambiri komanso mutha kupereka ndemanga pa

www.avantmalawi.com

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *