AMWENYE AKUPITILIZA KUPANGIRA NKHANZA AMALAWI

olemba Dr mwale

Miyezi iwili yapitayo Avant publications inalemba nkhani yokhuza company ina ku brantyre yomwe imapanga ufa kuti imawachitira nkhaza ogwira ntchito ake.

Koma lero tabwera ndi nkhani ina yofana ngati yomweyi yomwe yachitika ku Lilongweku area 4 komwe kuli company yomwe ikupanga nsapato(pafupi ndi mbc tv).
Kumeneku amweye akumawatsekera anthu ogwira ntchito mkati ndipo iwo akumatha kuchokapo ndi makiyi.

Chatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke mnyanga ndi chakuti dzulo mwachizolowezi bwanayo anatsekera ogwira ntchito mkati mwa fakitale imeneyi ndipo ali mkati mogwira ntchito fakitaleyi inayamba kuyaka Moto , pomwe anthu amaganiza zothawa anagwira njakata poti pakhomo panali potseka .

Bwanayo ataimbilidwa foni anathamanga ndikupeza kuti anthu awiri anali obanika kwambiri .

Chodandaulitsa ndichakuti mmalo moti anthuwa awatengere kuchipatala mmwenyeyu anauza anthu kuti aziwathira madzi anthuwo kwinako iye akupanga zopulumutsa katundu kusiya anthu akuvutika ndi ululu wa Moto. Izi zinatengera anthu ena kumukokera pa mbali mmwenyeyu kumuuza kuti anthuwa apite kuchipatala.

Kodi akanakhaka kuti iyeyo anali kutali ndi makiyi zikanakhala bwanji? Nanga akanakhala kuti ataika akanatani?

Pempho la anthu ogwira ntchito ku fakitaleyi ndi loti nduna yoonaza ma fakitale iziyendera mafakitale kuti pena azichezako ndi anthu omwe akugwira ntchito ndikukonza zomwe zikulakwika, “akamatilekerera nchonchi tikumapezeka kuti tikumazunzika ndi anthu obwera omwe akuika miyoyo yanthu pachiopyezo.” Adandaula chotero anthu omwe anatsina khutu avant

Nanu owoza za maufulu a anthu apantchito tadzukani pogwira ntchito yanu mwaukadaulo chifukwa amalawi akuzunzika mwakachetechete.

Avant yapeza kuti anthu ambiri akuvutika mmalo awo antchito ndi mabwana achimwenye ndipo boma likuchedwa kuchitapo kanthu. Kodi mukufuna muzachitepo kanthu wina atamwalira?

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *