NTOPWA FC IKUGULITSIDWA

by ebenezer

Atalengeza masiku apitawo kuti sakwanitsa kuthandizanso timu ya Ntopwa F.C, Isaac Jomo Osman yemwe ndimwini watimuyi wabwera poyera ndikutsimikiza kuti tsopano ali okonzeka kuigulitsa timuyi.

Jomo wati pakadali pano njira zake zonse zomwe zimamupezetsa ndalama zayima kaye ndichifukwa chake aganiza kuti agulitse timuyi ndipo aliyense amene akuyifuna akuyenera amupeze kuti akambirane naye.
Masiku apitawo, Alfred Gangata yemwe adali mwini watimu ya Masters Security komanso kampani ya Sable Farming anawonetsa chidwi chofuna kugula timuyi ndikupitiliza kuithandiza mu TNM Super League.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *