MPUNGWEPUNGWE KU KARONGA UNITED

By Vinjeru Ngwira

Msogoleri wa osewera mu team ya karonga united
Richard kayuni limodzi ndi osewera amzake ena 46 ati sakugwirizana ndi zomwe ena akufuna kuti chairman wa team yawo Innocent Mkweweka akayimilire pa masankho omwe achitike pofuna kupeza akukuakulu oyendesa masewera a Mpira wa mendo Ku Northern Region Football Association.

Osewerawa ati akuwona kuti Mkweweka akapita Ku NRFA ndiye kuti team yawo ithera pompo popeza ndiyemwe amayisamalira team yawo ya Karonga United

Kayuni wati iwo ngati osewera mpira mu Karonga United akutha kuwona mtsogolo lowala mpasi pa umtsongoleri wa Innocent Mkaweke

Chocho, osowera mu Karonga United ati apita kukakumana ndi committe yoyendesa mpira wa mendo ya boma la Karonga kuti aletse a Mkaweka kukayima nawo pa masankho a region omwe achitike mu December.

Ndipo osewerawa anenesa kuti ngati sathandizidwa Ku district committee, ndekuti apita kukadandaula Ku region committee.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *