SEVILLA A LANDLORD A EUROPA

By Dr Mwale
.
Mpikisano wa Europa watha dzulo pa 21 September pomwe timu ya
Sevilla   yagonjetsa timu ya  Inter Millan ndi zigoli zitatu kwa ziwiri.
kutanthawuza kuti timu ya Sevilla yakhala akatswiri a Europa kwa ma ulendo okwana 6.
.
Katswiri wa team ya intermilan Romelu Lukaku anayamba kugoletsa chigoli pa 5 minutes kudzera pa penalty, ndipo popomwe zimafika mphindi khumi ndi ziwiri katswiri wa Sevilla otchedwa De jong anamwetsa chigoli chofananila mphamvu.  Ndipo pomwe imafika 33 minutes de Jong adagoletseranso timu ya Sevilla, Koma timu ya intermilan inachinyanso pa 35 minutes  kudzera mwa katswiri Godin. Zomwe zinapangitsa kuti chigawo choyamba chithere 2:2.

  Lukaku wa timu ya inter Millan analodzensa mfuti anzake pomwe ana gunda mpira omwe umapita kunja, kuugundaku kunali kofuna kuuchotsa mpirawu zomwe zinapangitsa kuti mpira ukathere mu ukonde wa golo lake lomwe. Sevilla inagwiritsa ntchito mwayiwu po ntchinga kumbuyo mwa mphamvu kuti intermilan isapezenso chigoli zomwe zinathekadi.

Mawa kuli ma finals a UEFA champions league pomwe Bayern Munich ikumane ndi team ya psg.

Yemwe anali mphunzutsi wa team ya arsenal asern Wenger wati Chaka Chino champions league itenge ndi team yomwe sinatengepo kale, Kodi ndi psg?