ZILI PATI ZA MA RISK ALLOWANCE AAPHUNZITSI?

by Patrick Ngozo

Zambiri zakambidwa zokhudza kutsekulanso sukulu ndipo ambirinso apereka maganizo awo pankhani yaku tsiku lija ndi school.

Koma avant publication ikhonza kutsimikiza kuti mnyumba zowulutsa mawu dziko zitathirana/kusinthana mawu ndi aphunzitsi pankhani ya risk allowance boma panopa yapatsidwa masabata awiri kuti liyankhepo pazamadando aaphunzitsi.

Masabata awiri apitawo boma lidasinthana mawu moopsezana kukwelerana pachulu ndi bungwe la aphunzitsi llija amati TUM ponena kuti sapereka risk allowance kwa aphunzitsiwa. Koma …www.avantmalawi.com ikhozano kutsimikiza kuti General secretary wa TUM wauza aphunzitsi ake kuti asadere nkhawa chilichonse chikhala monga mwapempho yawo.

Akumchenga ati akutsatira ndondomeko zonse zomwe ogwira ntchito m’boma amayenera kutsata asanayambe kunyanyala ntchito. Iwo ati masabata awiri omwe aperekedwawa akangotha opanda kuyankhidwa adzamema aphunzitsi onse kuti asiye kugwira ntchito.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *