olemba: Dr Mwale
Bwalo la milandu ku lilongwe latulutsa pa belo anthu anayi omwe anali ogwira nchito ku MERA omwe ndi a Collins magalasi, Patrick maulidi, Bright mbewe komanso munthu wina wa business wachizimayi a Dorothy Shonga,
Magistrate Violet Chipawo mu chigamulochi chake wati boma silinapereke zifukwa zomveka zomwe zingapangitse kuti anthuwa asapatsidwe Belo ndipo monga kunena kuti anthuwa atha kusoneza umboni komanso kuti atha kunyalanyaza kumabwera ku bwalo la milandu mulanduwu ukayamba kumvedwa
Bwaloli lati anthuwa akuyenera apereke 500,000 aliyense komanso akhale ndi mboni ya ndalama zokwana 5million kwacha aliyense yomwe boma lizamange ngati anthuwa athawa,
Bwaloli lalamula kuti anthuwa apereke ziphatso zawo zoyendera, asatuluke chigawo chapakati osauza bwalo komanso azikaonekera ku police head quarters pa matsiku 14 alionse kufikira mulanduwu uzathe.
Mmene chigamulochi chimaperekedwa athuwa sanawatulutse nthawi yomweyo koma amayenera kutuluka 2 koloko masana bwalo likaunika zikalata zawo kuti awone ngati akwanilitsa zotse zomwe bwalo lanena ,
Ife tiitsatira nkhaniyi mwa chidwi mpaka kumapeto