ZOMWE ZIKUCHITIKA KU MEDF

Dr Mwale

MEDF ndi bungwe lomwe likupereka ngongole kwa ama business, kamba koti zonse zimayenda mundale bungweli nalo linalowa ndale munthawi ya boma lapitali pakagawidwe ka ngongole

Ku MEDF kukuoneka kuti ndalama zambiri zinasokonezedwa, zomwe zidapangitsa kuti boma la Tonse liimitse Kaye ntchito yopereka ngongole kwa anthu kuti bungweli lifufuzidwe.

Padakali pano ntchito yofufuza momwe ndalama zinayendera ili mkati(auditing) koma chomwe chikudabwitsa ndi chakuti konse komwe ma auditors apita ma regional manager komanso ogwira ntchito ena aku finance depatrment a MEDF akutsatira ma auditors amenewa ngati nawo ndi ma auditors.

Ma auditors akufunika agwire ntchito okha ndipo apatsidwe mpata olankhulana ndi ma loan officers mwaufulu ndikuwafunsa mmene zinthu zimakhalira.

Ma report omwe Avant publications yapeza akusonyeza kuti ma auditors sakupatsidwa mpata ndi ma official a MEDF pomwe akumakhala ngati ndi ma bodyguard awo.
Izi zikusonyeza kuti chilipo chomwe akubisa komanso kuopa kuti zingaziwike.

Pakadali pano Pali mphekesera yaikulu yoti ma auditors alandila 1 million aliyense kuti asaulure zenizeni zomwe zikuchitika ku MEDF

Pakadali pano boma lati MEDF iyamba kupereka ngongole pa 1september

Share this article

3 thoughts on “ZOMWE ZIKUCHITIKA KU MEDF

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *