By wongani Chipeta
Mtsikana wina wamdera la la Tembwe mmudzi mwa Maganga ku Mchinji wachotsedwa kubanja chifukwa chisakhutira ndi mwamuna wake. Mtsikanayu, Julia kamzere, anamagwitsa ukwati loweruka lapitayi pa 8August koma banjalo pano lasokonekera.
Avant publications yapeza kuti atalengeza ku mpingo wa Tembwe CCAP monga mwadongoso kwa sabata zitatu kudaonetsadi kuti kulibe oletsa kuti ukwati umangidwe ndipo ukwatiwo unamangidwa.
Zonse zinayenda bwino bwino ndipo akwati adatengana kupita kwawo kwa mwamuna. Atafika kwawo kwa mwamuna usiku banjali sadakhalire malo amodzi monga banja kamba koti mkazi amati adali watopa. Mwamuna adapirira mpaka kudacha. Mmawa mkazi adatenga phone kuyimbira chibwezi chake cha mmudzi momwemo mwa Maganga kuti mwamuna wake sadapaone.
Sunday madzulo mkazi sadavulenso zovala zake kumukana mwamuna mpaka Tuesday. Mwamuna anapeza mawu omwe mkaziyo amakambirana ndi chibwenzicho. Apa ndipamene zinthu zinavuta.
Mwamuna adayitanitsa nkhoswe, alangizi ndi mpingo kuti athandizepo. Dzulo la chinayi ndi pamene anthuwa anapita ndipo mkazi adavomera kuti adalidi pachibwezi ndi mamunayo ndipo wakhala akugona naye ngakhale nso litakhala tsiku limodzi kuti amange ukwati.
Mkaziyo akuti ndichibwenzicho chimene chimamuuza kuti asagonenaye mwamuna wakeyo .
Pakadali pano mkaziyo wabwerako kubanjako. Mamuna amagwira ntchito Ku Lilongwe ku company ina yapanga soya pieces.