UTM IKANA JOMO OSMAN

olemba Dr Mwale

Avant publications yapeza kuti Sipanathe miyezi isanu Tonse alliance chilowereni m’boma koma tikuona anthu ambiri achipani Cha kale cholamula akukhamukira kuzipani zomwe zinapanga mgwirizano wa Tonse.

Nkhani yomwe yatipeza kumene ndiyakuti National executive committee(NEC) ya UTM inalandira nkhani yoti JOMO OSMAN yemwe. ndi khansala wa DPP akufuna kulowa chipani Cha UTM. Akulu akulu a UTM atakumana agwirizana zoti asalolere jomo aka mtopwa 1 kulowa chipani chawo ponena kuti ndi munthu yemwe wabweretsa mbiri yonyasa muchipani Cha DPP ndipo wanzunza otsatira zipani za UTM ndi MCP mokwanira mu nthawi ya kampeni. ndipo www.avantmalawi.com kumulora iye kutha kukwiyitsa otsatira chipanichi.

Sitikudziwa kuti pano jomo alowera kuti Kodi mcp imulandirakapena angokhalabe ku DPP?

Zimenezi NEC ya UTM yachita zaonetsa kukula pa ndale chifukwa anthu ena amangofuna kukhala mbali yolamula yomwe sanaivutikire nkomwe komanso jomo atha kuchita izi pofuna kuti athawe milandu yomwe ali nayo.

Jomo ali ndi milandu yokwana 17 kupolice ndipo pakadali pano milandu itatu ndi yomwe inalowapo mu court

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *