THE MATTER WAS IN COURT

olemba dr mwale

Bwalo la milandu ku zomba lomwe lakhala likumva za mlandu wa a misonzi chanthunya omwe anapha bwenzi lawo a linda gasa( 25) .

Mtsikanayu anali wakuzimbabwe koma amaphunzira college ya polytechnic ku brantyre komwe anapalana ubwezi ndi achanthunya.

Avant publications yapeza kuti mulanduwu watha pafupifupi zaka 10 chifukwa chakuti ataphedwa nkaziyu a chanthunya anathawira ku South Africa komwe dziko lamalawi linagwilitsa ntchito police yaku dzikolo kuwagwira achanthunya.

Atagwidwa mzikolo mkuluyu amakana kuti abwere kuno ponena kuti amafuna kuti mlandu wakewo awumvere komweko koma boma linakana ponena kuti mlanduwo anapalamula kuno.

Chifukwa Cha ndalama zomwe zimapangitsa kuti azigula ma lawyer mlanduwu wakhala ukuimitsidwa kangapo koma boma linakana pempho la a chanthunya loti apatsidwe belo.

Lero bwalo lamilandu lapereka chigamulocho choti a chanthunya akhale kundende moyo wawo wonse komanso www.avantmalawi.com awagamula kuti akhalenso zaka zinayi mu ndende kamba kobisa mtembo komanso kubisa umboni.

koma chifukwa Cha chigamulocho chokhala kundende moyo wawo wonse zaka zinayizi zilibe kanthu.

Phunziro mlandu ungachedwe bwanji koma umatha basi

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *