Olemba DR MWALE
Avant publications musabatayi yakhala ikutsatira mwachidwi nkhani zosiyana siyana, komabe pamene Ndale zafika pokoma makamaka pa nthawi ino pomwe boma la DPP linachoka ndipo pano boma lomwe likulamula ndi la Mgwirizano wotchedwa Tonse Alliance momwenso muli zipani zokwana zisanu ndi zinayi. koma Zipani za MCP ndi UTM ndizo zipani zomwe zili ndi mphamvu mu mgwilizanowu. Koma mkatikati mwa zipanizi muli kagulu kena komwe kanatumphuka kotchedwa citizens for transformation (CFT) komwe cholinga chake ndikubweretsa kusintha mkaganizidwe pa ndale m’dziko muno.
DR MWALE amene ndi mmodzi mwa olemba nkhani ku Avant publications akutitengera ku chigawo Cha kumpoto komwee ku karonga komwe gulu la CFT tsopano lagawanikana, Komanso likufuna kugawanitsa MCP ndi UTM.
CFT idayamba ndi a Timothy Mtambo (Amene amadziwika bwino ndi dzina loti Comrade Mtambo) yemwe anali mtsogoleri wa bungwe la HRDC. Iye pamodzi ndi wachiwiri wake A Gift Trapence anabweretsa kutsintha pandale pomwe iwo anagwedeza Malawi ndi zionetsero zomwe amachititsa dziko lonse. A Mtambo anali munthu oti akayankhula zinthu zimachitika, zionetsero zawo zikamachitika kumakhala anthu ochuluka kwambiri kuposera misonkhano ya ndale.
Avanti imatsata bwino Cholinga chazionetserozo chimene kunali kufuna kuchotsa mayi Jane ansah pa mpando. Inde kunena mosabisa kunali kufuna kuchotsa chipani Cha DPP ndi utsogoleri wake umene amatsogolera ndi a Peter Muntharika ndipo khumbo la Mtambo linathekadi.
Atadziwa kuti tsopano zatheka angakhale Jane Ansah amakakamirabe pa mpando Mtambo anatsogolera Jane Ansah potula pansi udindo ku HRDC ndipo naye Jane ansah (mayi madando) anatsatira.
Tsopano Mtambo wachoka ku HRDC ndipo wapanga gulu lake lotchedwa CFT. Iye sanabise chichewa polankhula ndi amalawi ponena kuti tsopano CFT yasankha Tonse alliance kuti ndi yomwe tiithandize poipangira kampeni.
Nkhaniyi inatsangalatsa aliyense yemwe amachita nawo ma demo ponena kuti Mtambo abweretsa kusintha kwakukulu pa misonkhano yokopa anthu imene avant publications yakhala ikukupasirani. Ndipo DPP inadana nazo izi.
Koma ndizosabisa kuti a Mtambo mkutheka anali kale ndi chipani chomwe amachifuna kuti chidzapambane. M’mbuyomu panamveka mau ojambula omwe amamveka kuti a Mtambo amakambirana ndi yemwe pakadali pano ndi mtsogoleri wa dziko lino a Dr. Lazarus Chakwera kuti achita chotheka cholimbana ndi ulamuliro wa DPP kuti mpaka achoke. Apa ndi pomwe dziko lamalawi linadziwa kuti pambali polimbana ndi kumenyera ufulu wa aMalawi Comrade Timothy Mtambo anali ndi khumbo – khumbo loti chipani cha MCP chilowe m’boma.
A Cornelius Mwalwanda anamwalira ndipo chisankho Cha chibwereza Chimene Avant ikutsatira mwachidwi chikufuna kuchitika ku Karonga central.
Gulu lomwe silidziwika ngati lili la Ndale kapena ayi la CFT kuphatikizapo mwini wake Mtambo, akangalika kupanga kampeni ku Karonga ponena kuti “MCP ndi chipani chokhacho choyenera kuchipatsa voti, zinazi ayi.”
Mawu awa ayankhulidwa ndi munthu yemwe ali nduna mu boma la Tonse yemwenso ndi mtsogoleri wa gulu lomwe si lachipani koma lomenyera ufulu zinthu zikalakwika pa ndale a
A Timothy pagonachi sibenga Mtambo
Kodi MCP ikalakwitsa CFT ya a Mtambo idzatiimira aMalawi ngati HRDC?
Gululi tsopano lagawikana ponena kuti Tonse tinali ndi cholinga chothana ndi ulamuliro wa DPP koma enafe ndi a UTM ndipo ena ndi a MCP . A Mtambo apeleka support yawo kwa mwana wa a Mwalwanda ndipo achinyamata atsina khutu Avanti publications kuti ena akana kutero ponena kuti iwo akufuna A Frank Mwenefumbo a UTM. Kodi izi zikuthandauza chiyani ku gulu la CFT komanso a Mtambo?
Polankhulapo katswiri wina pa ndale a Manice abiti William danwood ati “ndine odadwa kuti anthu akuti ndichifukwa chani Mtambo akupanga kampeni ya MCP? Uyuyu ndi wa MCP kuyambira kale, za chipani chake Kaya movement yake ija zinali zabodza chabe ankangofuna kukuputsitsani anthuni, Mtambo ndi wa MCP.”
Ndipo naye mtolankhani wa Avant publications Deus Sandram obwande wati “inenso kulankhula mwachilungamo ndine odadwa kuti anthu akudabwa kuti a Mtambo akusapota MCP. Iye ananena kale kuti ndi wa MCP ndipo iye kupanga kampeni wa MCP chisakhale chipsinjo ayi. Kumbukirani kuti iye anadzichotsa mmaudindo onse omwe analimo omwe akanatha kumutchingira kupanga ndale ngati kuchoka ku HRDC ndipo pano iye ndi wandale basi atha kupanga zomwe akufuna. Bungwe lake lija ndi la ndale nde musiyeni apange ndale komanso kampeni mwaufulu ndipo yemwe apambane apambane basi.
Nawo a Wongani Chipeta omwe amalemba nkhani za ndale ku nyumba yomweyi ya Avant publications ati “kuchita ndale kwawo sikondabwitsa koma malankhulidwe a Mtambo atha kudzetsa www.avantmalawi.com kugawanikana mu boma la Tonse chifukwa iwo ati mtambo analankhula “kuti voterani MCP chifukwa ndi chipani chokhacho choti chingavoteredwe mubomali”. Ndikuona ngati akanangotambasula mfundo za chipani chawo osalimbananso ndi UTM ayi”.
Anthu ena angapo omwe ati tisawatchure maina awo auza Avanti publications kuti a Mtambo ali ndi zokhumba zambiri pa ndale angakhale anthu akungoona ngati akumenyera ufulu wa amalawi ,anthuwa ati mtambo akufuna kudzaimira pa u president koma ngati sazitenga bwino kutchuka kwake kuthera mmalere chifukwa akuchita zinthu mwa changu kwambiri.
Vinjeru Ngwira komanso yemwe amadziwika bwino kuti Ebenezer awiriwa agwirizana maganizo awo ponena kuti, “Comrade Mtambo analakwitsa kuuza gulu lake kuvala ma uniform a gulu la CFT kumisonkhano ya chipani ponena kuti otsatira gululi ndi azipani zonse zomwe zili mu Tonse (UTM/MCP), nde poonetsera mawanga kuti mtsogoleri wawo ndi wa MCP iwonso sanachedwe koma kupita kuchipani chapamtima wao Cha UTM. Kodi zimenezi sizisokoneza ntchito za bungwe lomwe silachipani? Nanga achinyamata ena omwe sakupanga zofuna za bwana wawo sachotsedwa mu gululi?”
Greshum Chikoti yemwe amagwira ntchito ya utolankhani ku Avant publications koma wakhala akutsatira kwambiri ndale kuchokera pomwe kunayamba kuchitika ma demo wati atsogoleri awiri a UTM ndi MCP amagwirizana koma zomwe zikuchitikazi zikufuna kubweretsa mpungwepungwe mu boma la Tonse ndipo gwero la mpungwepungwewu litha www.avantmalawi.com kukhala bungwe la CFT ndi mtsogoleri wake Mtambo, ndipo iye wapempha zipani zonse kuti zisatengere zomwe bungwe la CFT likuchita chifukwa zitha kusocheletsa aMalawi.
Nali pempho kwa Comrade Timothy mtambo: “Musabweretse chisokonezo mu boma la Tonse, kuli bwino kubwera poyera ndikunena kuti Inu ndi wa MCP, okutsatirani akutsatireni mwa kufuna kwawo. Ngati mukufuna chipani lembetsani bungwe lanu ngati chipani koma funso kumati mukwanitsaaaaa?”
Tsatirani
www.avantmalawi.com
Ndikuwerenga nkhani mwakathithi
DR MWALE