PROPHET SABAO ATULUKA KUNDENDE

By Dr Mwale

Mneneri odziwika bwino komanso yemwe ndi mwini wake wa Mpingo wa    Avangelic Gathering Church(AGAC) Prophet sabao atulutsidwa kundende.
Asabao anamangidwa ndi boma la dpp kamba koganizilidwa kuti adaba ndalama zosaposera 3 million ku account ya munthu yemwe amapanga naye business limodzi(zikumveka kuti anali Apongozi awo)

Malingana nkuti mneneriyu ananenera zoti DPP iluza chisankho ndipo MCP ipambana boma la DPP linanyasidwa naye mneneriyu ndipo mwayi wa mlandu utapezeka sanamumvere chisoni koma kumulamula kukakhala kundende kwa zaka khumi.

Koma mwa chisomo Cha mulungu zonse zomwe ananenera zinatheka ndipo pano DPP inatuluka muboma,.ndimphamvu zomwe president anapatsidwa zoti atha kutulutsa akaidi ena, president chakwera watulutsa akaidi okwana 499 pofuna kupewa mlili wa covid19 mundende za mdziko lino ndipo apa achakwera akumbukira kuti mneneri sabao yemwe ananenera za ufumu wawo ali mundende ndipo iwo alamula kuti akhale mgulu la anthu otulutsidwa(maloto a yosefe)

Mwachudure a sabao ananenera kuti MCP iwina koma sizikhala zophweka koma ulendo uno kumwamba kwakana, iwo anati DPP ichita chotheka kuti iwine koma sizitheka, mlandu wachisankho usanayambe iwo ananenera kuti mulungu wakwiya ndipo atumiza mngelo kukavumbulutsa zobisika zomwe zimachitika mu ma computer a MEC, apatu nkuti suleman asanadziwike ndipo zonse zinachitika monga ananenera, zachisoni pomwe timavota ndikulandira ufuluwu nkuti iwo ali mundende.tiyamikire mulungu kuti lero atuluka.
Ngati asabao analagamulidwa kukakhala kundende zaka 10 kamba ka ndalama zosapisera 3 million kulibwanji omwe anampha munthu komanso kuba ma billion?

Kutuluka kwa a sabao kwadzetsa chimwemwe kumpingo wawo.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *