OLEMBA DR MWALE
Anthu omwe amakhala pa chilumba Cha likoma lero agwira njakata pomwe oyendetsa sitima waledzera kotheratu
Sitimayi imayenera kunyamuka lero mmawa kupita pachilumba Cha Likoma ndipo team ya motal engil itaona kuti zonse zili bwino ndipo akuyenera kunyamuka ndipamene anazizimuka poona kuti oyendetsayu waledzera moti sakanatha kuye detsa anthu pa Nyanja.
Anthu omwe amapita ku Likoma awonetsa kukhumudwa kwawo pomwe amalankhulana ndi Avant publications. Titayesera kulankhuka a ndi olankhulira motal engil a Thomas chafunya kuti timve zambiri pankhaniyi koma phone yawo simapezeka
Tikupempha amotal engil kuti azikhala ndi oyendetsa angapo pa malendo awo komanso apereke chilango kwa oyendetsayu chifukwa atha kuzaphetsa anthu ndi mchitidwe wake oterewu