*NANKHUMWA AYITANISIDWA KU KOMITI YOSUNGITSA MWAMBO

olemba Dr mwale

President wa chipani Cha DPP mchigawo chakumwera yemwenso ndi mtsogoleri wachipani chotsutsa mnyumba  ya malamulo a Kondwani Nankhumwa aitanitsidwa ndi chipani Cha  DPP kuti akawafunse mafunso pa zinthu zomwe akuti anankhumwa alakwitsa mchipanichi.

Mkalata yomwe www.avantmalawi.com yaona yati a Nankhumwa akufunika kukayankhapo mafunso pa nkhani ziwiri.
yoyamba ndiyakuti anankhumwa anakumana ndi akulu akulu a chipani Cha MCP makamaka mayi Cecelia kadzamira osawadziwitsa a muthalika komanso Nec ya DPP ndipo nkhani yachiwiri ikukhuzanandi zamaphunziro awo a nankhumwa zomwe zakhala zikumveka kuti anankhumwa akugwilitsa ntchito certificate ya m’bale wawo osati yawo.

Malingana ndi kalata yomwe alemba a Charles Mhango monga mlembi wa komiti yokhazikitsa mwambo ku chipani Cha DPP akuti msonkhanowu uchitika mawa 10 am ku Golden peacock ku Lilongwe

Avant publications izatsatila bwino lomwe mkumanowu ndipo tikupatsirani zonse mawa.

Kuti musatire zonse onani pa www.avantmalawi.com

*DR MWALE*

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *