olemba Dr Mwale
Sabata yapitayi pa social media panali uthenga omwe umaonetsa kuti company ya tnm ikufuna kulemba achinyamata ntchito ngati gawo limodzi lothandizira kulemba achinyamata ntchito.
Lamulungu olemekezeka a msungama anakumana ndi achinyamata pa school ya chioko ku chilinde komwe anawauza kuti a tnm ali ndi mwayi wanchito ndipo pakufunika achinyamata omwe anapangapo maphunziro a ku college, polankhula motsindika msungama anati aliyense amene akuziwa mzake yemwe ali ndi pepala lapamwamba amudziwitse, ndipo lamulungu Mpingo nayo monga CCAP ya mmalimana ku chipasula inalengeza za uthenga omwe andunawa amalengeza zomwe zinapangitsa kuti lero ku chioko school kukhale chigulu Cha achinyamata a mapepala oposera pa msce ndi chiyembekezo choti alembedwa ntchito.
Zachisoni a tnm atabwera anauza achinyamata kuti I wo amafuna munthu aliyense yemwe ali ndi smart phone kuti azigulitsa ma simcard www.avantmalawi.com tikuti achinyamata a ma diploma azigulitsa ma simcard.
Anthu anakwiya kwambiri ndipo ambiri anabalalika osamva nawo zomwe zinalikozo.
Achinyamata panopo akufuna chochita nde musamawatengere kowayesa chifukwa ulova wakula kwambiri