MPINGO WA ASSEMBLIES OF GOD UGONJERA M’BUSA WA PAMALO

olemba – Dr Mwale

Titha kutsimikiza kuti Mpingo wa Assemblies of God mu ulamuliro wa a Rev Chitsonga uli ofooka pakudzudzula komanso kulangiza a zibusa amene khalidwe lawo sili lopereka Ulemu kwa Yehova.

Izi zatsimikizika pamene a Khristu a Mpingo wa Chinamwali Assemblies of God anagangalama mkuthamangitsa amene anali M’busa wa pamalopo Langston Muva. Tafotokoza kuti amene anali M’busa pakuti pakadali pano ma report otsimikizika akuonetsa kuti a Muva akusithana ndi Rev Mvula amene amatumikira ku Liwonde Assemblies of God.

Ngakhale utsogoleri wa Assemblies wakakamizidwa kusinthaku ndi mamembala ake, utsogoleri wa mpingowu wawonetsa kufooka pakumvera Bishop Muva, amene amamuopa pakuti ndi mmodzi mwa anthu amene akhala mu Assemblies of God nthawi yayitali.

Mukafukufuku wotsimikizika akuonetsa kuti a Muva adathamangitsidwapo ku Kanjedza, ku Mzuzu komanso ku Area 23 ku Lilongwe pakhalidwe lawo lonyozetsa Mpingo.

A busa a Muva adamanga nyumba Ku Songani, ku Zomba Zomwe zidapangitsa kuti akane kupita kutali ndi boma la Zomba kuopa kutalikira ndi Nyumba zawo (Zoseketsa kwa azitumiki a Masiku ano, amene safuna kutumidwa ndi Yehova kumakana komwe mulungu wawatuma chifukwa choti ndi kumudzi kapena sakapeza zokhumba za mtima wawo)

Utsogoleri wa Assemblies of God pogonjera a Muva udayesetsa kuwapititsa ku Chigonjetso Assemblies of God – Mtauni mweni mweni mwa Zomba (komwe kukutumikira Rev M’bwana). Koma a Khristu akumeneko adatemetsa khwangwa pa mwala kuti sangalandire abusa akhalidwe lochititsa manyazi. Komanso izi zagwedeza ubale wa abusa a M’bwana ndi akhristu awo, pamene a Khristu alamula M’busayo kuchoka pamalopo pomunena kuti ndi ozikonda, osayamika komanso okonda ndalama (Chifukwa analolera kupita ku Mpingo komwe kuli makobili.)

Izi zinapangitsa kuti utsogoleri wa Assemblies ku chigawo chakum’mwera, usowe mtengo ogwira ndipo uchotse A Rev Mvula (aku Liwonde) kusinthana ndi a Muva (aku Chinamwali Assemblies of God).

Ngakhale zili chomwechi, koma talandira ma report kuti utsogoleri wa Chinamwali Assemblies of God ukukana kulandira a Busa a Mvula amene anachoka ku Mangochi mothamangitsidwa mbuyomo.

Kodi tiziti azibusa a Assemblies onse ngosokonekera mmakhalidwe awo?

Uthengawu ukuyenera kufika kwa President a dziko la Malawi kuti ayitanitse azibusa anzawo ndikukambirana za mmene azibusa a Mpingo wawo akuipitsira mbiri ya Mpingo wawo yomwe imayenera kukhala yowala chifukwa ndi Mpingo wokhawo womwe watukutsa m’busa yemwe pakadali pano akuyendetsa dziko lino, izi kuzilekerera zitha kuipitsa mbiri ya mtsogoleri wa dziko lino ngati kuti naye anali m’busa wachinyengo ngati enawa komanso kuti akupemphera mpingo osalongosoka.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *