MGWILIZANO WA UDF NDI DPP WATHA

olemba DR Mwale

Tsopano Avant publications itha kutsimikiza kuti Chipani Cha UDF chalengeza kuti ubale wawo womwe unalipo pakati pa zipani ziwirizi(UDF/DPP) tsopano watha.

Titaluza chisankho Cha pa 23 June tsonapo tonse tili kotsutsa boma nde palibenso chifukwa chokhalira mu mgwilizano.
Pakadali pano ngati www.avantmalawi.com Pali ma mapulani okhalanso mu mgwilizano ndi chipani chilichonse zonsezi zioneka mtsogolo koma pakadali pano chipani Cha UDF ndi choima pachokha.

Izi zikudza pomwe muchipani Cha DPP mulibe mgwilizano pomwe akulu akulu odalilika akuchotsedwa mmaudindo komanso ena kutula pansi kamba kosamvana chimodzi pa yemwe akuyenera kutsogolorera chipanichi. Chipani  Cha UDF chinalowa mu mgwilizano ndi chipani Cha DPP kumayambiriro a Chaka Chino bwalo la milandu litalengeza kuti chisankho Cha president chichitikenso ndipo owina azizapeza ma vote oposera 50+1

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *