MA CHURCH SAKUTSATILA MALAMULO A COVID19

olemba Dr Mwale

Boma la Malawi kudzera mu bungwe lomwe a president anakhazikitsa kuti liziona  kapewedwe kamatenda a covid19 la presidential task force likuyenera kuchilimika ndikugwira ntchito yoyang’anira Madera osiyanasiyana kuti aziona mmene anthu akumachitira malingana ndi lamulo loti anthu asamasonkhane ochuluka mmalo opempherera komanso mmaukwati.

Avant publications  itayendera malo opempherera kumapeto kwa sabatayi yapeza kuti mipingo ndiye ili patsogolo kuphwanya malamulowa monga a www.avantmalawi.com atolankhani anthu anayendera Mpingo wa sevethday Adventist pa 29 September  2020 ku balaka komanso mpasa 2 CCAP ku phalombe komwe tapeza kuti anthu akupemphera ngati kale, kulibenso Zija zosamba mmanja, kuvala ma mask   komanso Church linali lodzadza ngati kulibenso matenda a Corona.

Ife monga Avant publications tikupempha boma kudzera mu unduna wa zaumoyo, unduna owona za mdziko komanso presidential task force kuti aziyenderako Madera ena ndi nena maka maka malo opempherera, maukwati komanso ma party kuti anthu azitsata malamulo.

Ngati anthu ogwira ntchito akuchepa iyi nde ntchito yeni yeni ya thandizo la ndalama za covid19 zomwe dziko lathu linalandira lembani anthu azigwila ntchito imeneyi mmaderamu.

Ampingo nanu moyo mulinawowo si wa boma ndi wanu nde usamalileni.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *