mulembi: Dr Mwale
Chitengereni boma a mgwilizano wa Tonse president ndi wachiwiri wake akhala busy kukonza zinthu Zina zowwe eni ake akuti zinasokonekera komanso kuti sizimayenda bwino mu ulamuliro wa DPP pansi pa president Peter Mthalika.
Anthu ambiri asinthidwa mmalo awo ogwirira ntchito komanso ena akwezedwa ma udindo pamene ena atsitsidwa, pomwenso ena achotsedwa ntchito ndikulemba ena.
Nkhanyi yomwe yachitika lero ndiyoti alembi kapena kuti ma secretary ambiri achotsedwa ntchito ndikuikapo ena atsopano, monga mndandanda wa alembi omwe achotsedwa ntchito omwe Avant Publications yaona uli motere.
- Lucky Sikwese tsopano ndi mlembi wa foreign affairs I wo alowa mmalo mwa a Ben Botolo omwe pakadali pano sitikudziwa kuti apita kuti.
- Mr chimota mlembi wa ku Human resource wachotsedwa ndipo mmalo mwake mwalowa Mr chimbalanga (opuma kale pa ntchito) ndipo sizikudziwika kuti a chimota apita kuti tsopano.
- Ku unduna wa zamaphunziro nako mlembi wa kumeneko a Mr saidi abwerera ku OPC (office ya president) ndipo mmalo mwawo mwalowa a chikondano kadzamira(Mrs mussa)
- Mr Peter simbani pano ndi mlembi waku industry kutsatira kukwezedwa kwawo pa ntchito.
- Mr sandram Maweru,amenewa achita kuitanidwa kamba koti anali atapuma pa ntchito koma boma lawabwenzeretsanso ndipo ndi mlembi waku irrigation.
- James chiusiwa pano ndi komishonala wa disaster manament affairs kulowa mmalo mwa Elvis Thodi omwe tichite kuuzidwa komwe akulowera.
- Christina Chatima Zakeyo tsompano ndi mlembi waku trade yemwe walowa mmalo mwa Dakamau yemwe wapita ku education ngat chief Director
- Joseph mkandawire apita ku natural resources ngati mlembi kumeneko.
- Jean munyenyembe pano ndi accountant general kulowa mmalo mwa Sungani Mandala yemwe sitikudziwa kuti boma limupititsa kuti
- A Patrick zimpita pano ndi a lembi aku transport and public works kulowa mmalo mwa Francis Chinsinga yemwe wapuma pantchito posachedwapa
11, Pakadali pano zatsimikizika kuti Charles Mwansambo ndi mlembi ku unduna wa zaumoyo ndipo a Dan Namalika atsitsidwa udindo tsopano ndi a director of health services

Mmene zikuonekera kusinthaku kwangoyamba ndipo kukupitilira koma zikudabwitsa kuti anthu omwe anapuma pantchito akumawaitananso mmalo motenga anthu omwe ali mu system kale ndicholinga choti mmalo awo boma lizilemberapo anthu ena ntchito.
Let’s not waste time ,remove all those cadets and let others enjoy the warm heart of Africa too, thumbs up that Dan namalika has been demoted, the lier