KUNALINJI KU NYUMBA YA MALAMULO

OLEMBA DR MWALE

Kachiwiri mu mbiri ya Malawi president wadziko lino wa chinamba 6 anakaonekera ku nyumba ya malamulo kuti akayankhe mafunso okhuzana ndi zomwe iye analankhula potsekulira nyumba ya malamulo. President woyamba kuchita izi anali DR Bakili muluzi wa chipani Cha UDF.

Atatsekulira paliyamenti mwandondomeko yake amayenera kuyankhapo ndi mtsogoleri otsutsa mnyumbayi ndipo apa anayankhapo ndi a Nankhumwa ndipo Avant publications inali konko.

Anankhumwa anati iwo akudabwa kuti boma la tonse silukupereka ndalama za ukaziotche (risk allowance) kwa aphunzitsi chifukwa chani? Anankhumwa anati aphunzitsi ndi ofunika kwambiri choncho boma la Tonse likuyenera kuwasamalira.

koma chakwera anawayankha anankhumwa kuti asaoneke abwino lero chifukwa iwo akhala m’boma zaka pafupifupi 12 anawapatsapo allowance aphunzitsi? Mesa munatseka school ndinuyo bwanji osawaganizira aphunzitsi? Musakhale abwino lero chifukwa choti muli ku opposition, chakwera anawauza anankhumwa kuti asamanene kuti boma la Tonse lakhala miyezi itatu ayi chifukwa kuchoka June kufika lero ndi matsiku 75 okha.

anankhumwa anatinso iwo akufuna achakwera atengere ulamuliro wa mtsogoleri yemwe anayambitsa chipanichi a kamuzu Banda. koma chakwera anawauzanso anankhumwa kuti mukamalankhula muzitsatira history chifukwa kamuzu Banda sanayambitse chipani Cha MCP koma aphungu otsutsa onse anazuma haaaaa! www.avantmalawi.com apa chakwera anapitiliza kuwauza kuti chipani Cha MCP anayambitsa ndi amalawi kamuzu anasabwete ndipo president wake oyamba anali Orton chirwa. koma kamuzu ndi tate wa fuko lamalawi pokhala president woyamba wa dziko. Aphunngu ambali ya boma anaseka ambali yotsutsa uku akuombera mmanja.

Chakwera anaoneka wa siliyasi kusocheza kuti amadziwa zomwe akuchit. chakwera anayankhapo pa zomwe ananena a Nankhumwa kuti boma lisamange nyumba za aphunngu mmadera mwawo, koma kuti amange nyumba za anthu ogwira ntchito m’boma monga apolice,aphunzitsi,asilikali komanso a zaumoyo ndi nthambi Zina za boma, koma chakwera sanachedwe kuuza paliyamenti kuti chifukwa chomwe iye akumangira nyumbazi ndichakuti boma limaluza ndalama pafupifupi 56 billion kulipira nyumba za aphunngu mtown mmalo moti azikakhala ku Madera komwe anawasankhira iye anati kutero boma lipulumutsa ndalama zokwana 700 billion pa chaka zomwe zipite ku magawo ena achitukuko komanso iye anati wathokoza kwambiri a Nankhumwa pozindikira kuti anthu onse omwe atchulidwa kuti akufunika kuti azikhala mmanyumba abwino alibe mmanyumba apa iwo akusonyeza poyera kuti zaka 13 zomwe iwo alamula dziko lino sanawasamale anthuwa powamangira mmanyumba nanga amapanga chani? Ndipo lero zakoma pati kuti azitiuza ife omwe tangotha matsiku 75 muboma? Pena ukamakhala mutogoleri otsutsa uziona Kaye zomwe boma lako lachita chifukwa apa simukuuza ife koma mukuzuzura boma lanu pa zomwe lalephera kuchita.

Chakwera wati boma la DPP linalephera kusintha Malawi kukhala ngati Singapore nde mudikire ife zomwe tichite.

Anankhumwa anafunsanso funso lina lomwe anati tikudabwa kuti Kodi akulamula bomali ndi Tonse alliance kapena MCP? Iwo ati anafunsa funsoli chifukwa choti mfundo zonse zomwe akulankhula a Chakwera zikungochoka kwambiri pa nsanamira za high 5 wa MCP, koma poyankha chakwera anati choyamba mudziwe kuti high 5 ndi mfundo zanji ndipo zonse zomwe mungatchule zili mkati mwa super high 5 ,monga utsogoleri otumikira anthu, kuthana ndi katangale , kutsatira malamulo, kagwiridwe kantchito kabwino ka anthu , komanso kuyendetsa boma bwino. nde mukaonetsetsa mfundo zonse za zipani zomwe tili nazo pa mgwilizano nazo zikukambaza zinthu zomwe zili mu fundo zomwezi kusonyeza kuti high 5 ndi ambulela yomwe pansi pake Pali mfundo zonse za mgwilizano wa(apa chilima pomwe anakhala anavomereza mfundoyi) Tonse nde kuyankhapo funso lanu ndi kwakuti ili ndi boma la Tonse ngati enanu muli ndimaganizo oti Tonse alliance igawanikana mukunama ndipo sizitheka ine ndi chilima ndi anzanga onse tikupanga chimodzi ndichifukwa chake kuno ku paliyamenti tabwera limodzi.mgwilizano wa Tonse simungaugwedeze chifukwa popanga zinthu timapangulira limodzi komanso choti mudziwe mulungu ndi wabwino nthawi zonse.

Chakwera atathana ndi Nankhumwa aphungu ena nawo anafunsanso mafunso monga kufunsa za fetereza otchipa kuti Kodi anthu sazapanga chinyengo pakagulidwe kake?
Poyankha Dr chakwera anati boma lawo liika ndondomeko yoyenera ndipo azizagwilitsa ntchito chiphaso Cha unzika kulowetsa mumakina a kompuyuta (computer) kupanga (swipe) kuti munthu agule fetereza ndipo kungopezeka wina akupanga chinyengo boma langa silizalekerera ndipo lamulo lizagwira ntchito.
Pankhaniyi yazaumoyo iye anati zipatala za matenda akhansa azitsekulira posachedwapa.

Aphunngu ambiri angakhale otsutsa boma anakhutira ndi zomwe analankhula president chakwera chifukwa pomwe mutogoleri wa www.avantmalawi.com nyumbayi anauza speaker wa nyumba ya malamulo kuti awuze aphunngu kuti avomereze zolankhula za president SONA aphunngu achuluka anavomereza koma ochepa omwe samakhwana ndi khumi anakana . Tsatirani zambiri lero pomwe budget ikuperekedwa ndi ndina ya zachuma a Felix mlusu. kuyambira 9:30 am pa www.avantmalawi.com

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *