KULIMBANA NDI KACHILOMBO KA CORONA KU ZOMBA

By Dr Mwale

Boma lamalawi silikugona tulo polimbana ndi kachilombo ka Corona komwe kakuyambitsa matendawa a covid19.

zomba depot

Tikunena pano m’boma la zomba anthu omwe akugwira ntchito yopopera mankhwala lero akupopera mtown imeneyi. Mmalo omwe apoperedwa ndi zomba Central market, free market , mu Depot komanso magalimoto onse ochita malonda onyamula anthu monga ma minibus ndi ma tax nawo apoperedwa.

Mu bus

Malingana ndi khonsolo ya zomba akuti  kupoperelaku kuzichitika  sabata iliyonse kuti alimbane ndi kachiromboka.

Ntchito ngati yomweyi inayamba kuchitika  mzinda wa lilongwe miyezi itatu yapitayo koma tsogololo la ntchitoyi silinaoneke komwe linathera.

Zikanakhala bwino kuti boma Lili lonse lizichita ngati mmene achitira ku zomba kuti tipewe kufala kwa kachiromboka TONSE ngati dziko.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *