FAM ISUMILIDWA

olemba Dr Mwale

Munthu wina yemwe ndi mzika yaku Malawi kuno koma amakhala kuja wasumira bungwe la FAM ku ACB, kuti afufuze zachinyengo zomwe zinachitika pa chisankho cha FAM.
Munthuyu wafotokoza kuti anthu ena anapatsidwa magalimoto, kupatsidwa ndalama ndikugulilidwa ma plasma.
Koma mkulu wa ACB Renic Matemba, wati awunika dandaulo lamkuluyu, koma iye wati pali kukopa kosiyanasiyana komwe anthu amachita kuti avoteredwe zomwe sizoletsedwa. Iye wati bola izi zichitike tsiku lachisankho lisanafike.
ACB yati ifufuza ndi zotsatira zakufufuza kwawo zituluka Lolemba sabata yamawa.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *