CHILIMA ATHETSA MKANGANO WA ESCOM NDI EGENCO

olemba: Dr Mwale

Lero vice President wa dziko lino a Saulosi Chilima anakumana ndi ma Kampani opanga magetsi kuphatikizapo bungwe la MERA.

Pa 22 July 2020 Chilima anakumana ndi ESCOM komanso EGENCO kuti akambirane mmene magetsi angakhalire mu zaka ziwiri opanda vuto lililonse ndipo kunali ku meeting komweku komwe a Dr Chilima anapeza kuti Pali kusagwilizana komwe kulipo pakati Pa ma kampani awiriwa, ndipo Chilima anapanga chotheka kuti akumaneso ndikuthandizana kuthestsa mavutowa kuti dziko lipitilire kulandira magetsi okwanira.

Mwazina kampani ya EGENCO inapereka madandu ake omwe akulepheretsa kuti isamapange magetsi okwanira zomwe ndi kuphatikizapo ma billions ochuluka omwe ESCOM ikulephera kulipira EGENCO Pa magetsi omwe ESCOM yakhala ikutenga Pa ngongole.

kusamaliza kwa malo ake ogwirirako ntchito omwe EGENCO ikumanga ndipo izi zinapangitsa kuti kampani ya EGENCO ikhale yopanda malo ake a umwini ogwilira ntchito.

Mbali inali ESCOM naye inapereka madandu ake monga kunena kuti kampani ya EGENCO ikuma charger ndalama zochuluka kuposa mmene zimafunikira, iwo ati EGENCO ikuonjezera 1.8 billion mwezi ulionse pamwamba Pa ndalama zomwe ESCOM imayenera kulipira, ESCOM yati EGENCO sikuphatikizira bwino ndalamazi ndipo iwo sakuyenera kupereka ndalama zochuluka chonchi.

Mavutowa azachumawa akhala akusokoneza ntchito za magetsi pomwe ESCOM ikutsutsa kuti ndalama zomwe EGENCO ikufuna zikuchuluka ndi 50% (pafupifupi theka)

Wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino atamva za mavutowa sanakukhale chete koma kuitanitsa mkumano ndi nthambi zonse za boma zokhudzidwa komwe anapanga chiganizo chofuna kutukula Malawi kuti apititse patsogolo ntchito za magetsi.

Lero Chilima walengeza kuti kusagwilizana komwe kunalipo pakatai Pa ma kampani awiriwa tsopano kwatha ndipo mavutowa akhala mbiri ya kale kuyambira lachisanu la sabata ya mawa ,izi tikuthandauza kuti boma libwenza ngongole zonse za ESCOM komanso kuthandiza kuti EGENCO imalize ntchito zake zomangamanga.

Lachiwiri asungi chuma aboma akumana ndi nthambi ziwirizi kuti athane nawo malingana ndi zomwe akambirane, Chilima wati ngati tikufuna dziko kupita chitsogolo tikuyenera kukumana ndi mavuto

Chilima wati Pa zomwe akambirane zambiri sangaziulule Kaye koma chomwe anganene pakadali pano ndi chakuti ESCOM isiya kugulira mafuta a diesel company ya Aggreko kuti izipanga mphamvu ya magetsi yomwe imakagulitsanso ku ESCOM, chomwe chimachitika ndi chakuti kampani ya Aggreko imapanga magetsi a mphamvu ya ma generator ndipo mmalo mogula okha diesel iwo amafunaso ESCOM kuti iziwagulira mafuta kenako kumawagulisanso magetsi, (business yanji imeneyi?) Kampani ya ESCOM yapatsidwa matsiku 30 kuti ikambirane ndi Aggreko za nkhaniyi ndipo ESCOM ayiuza kuti ipewe kusaina ma contract omwe sangawapindulire.

Chilima wati tsopano chatsala ndi chakuti ma kampani awiriwa apange dongosolo lomwe lionetsetse kuti magetsi asamavute mmalawi muno kwa zaka ziwiri zikubwerazi.

Tsogolo lathu lowala lafika watero Chilima mkumaliza kwake.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *