Olemba Dr Mwale
Bwalo la milandu la Chikwawa First Grade Magistrate pa 13 August 2020 linalamula achinyamata atatu kuti akakhale ku ndende kwa miyezi 18 kapena kupereka chindapusa Cha Mk 500,000 aliyense komanso kupereka ndalama yokwana Mk 100,000 yomwe a bwalo la milandu awononga pa mlandu womwe achinyamatawo anapalamula woseweretsa komanso kuwononga ndalama
.
Achinyamatawo pa 13 July 2020 anajambula kanena/ video yomwe imkawonetsa achinyamatawo ali ku malo komwelako mowa ndipo amkaseweretsa ndalama za pepala ma 2,000 pomwe ndalama zina amkazidya pomwe zina anazimata kuma botolo a mowa ku Ngabu trading centre.
.
Achinyamatawo anakawonekera ku bwalo la milandu komwe anapezeka olakwa pa mlandu wowononga ndalama.
Bwalo la milandu linalamula achinyamatawo kupereka chindapusa Cha Mk 500,000 aliyense kapena kupita ku ndende kwa miyezi 18 komanso linawuza achinyamatawo kupereka ndalama yokwana Mk 100,000 aliyense zomwe bwalo la milandu lawononga poyendetsa mlanduwo koma pakadali panopa achinyamatawo apereka aliyense Mk 600,000.
.
Achinyamatawo ndi a Rodrick Bwanali a zaka 21, Dani Soza a zaka 33 ochokera m’mudzi mwa Robert ndi Willy Paimva wa zaka 23 wochokera m’mudzi mwa Goma onsewo ochokera dera la mfumu Ngabu m’boma la Chikwawa.