Amangidwa chifukwa choononga katundu

olemba wongani Chipeta

Apolisi mboma la Mchinji amanga anthu ena pamalo a malonda a Bua Trading Center kamba koononga ndi kuba katundu wa munthu wina pomuganizira kuti anali wakuba.

Lachiwiri lapitali mkulu wina amachokera ku Mozambique kusamukira kuno ku Malawi. Pochoka ku Mozambique analipira galimoto kuti akanyamulirepo katundu wake. Katunduyo anali mbuzi 49 ndi akalulu.

Pofika pa Bua Trading, Avant publications yauzidwa kuti mkuluyo anali atalumikizana ndi mkulu winanso wagalimoto kuti akamulandilire ziwetozo. Anafika pa Bua usiku kwambiri anthu atagona.

Popeza unali usiku kwambiri anthu ena atawona galimotozo zitaima eni ake akutsitsa ziwetozo anaganiza kuti zinali mbava. Izi zinapangitsa anthuwo kumemeza anzawo kuti akagwire anthu oganiziridwa ndi umbavawo.

Atawagwira anthuwo anthu anayamba kuwononga magalimoto ndi zida zosiyanasiyana. Ena anali akutenga zowetozo nkuthawitsa, ena kuba ma battery agalimoto ena matayala amene. Kuonjezera apo anawononga galimotozo moti sizingayendenso.

Nkhani itafika kuPolisi ndipamene zinadziwika kuti anthuwo sizinali mbava koma anali mkulu wosamuka kuchoka ku Mozambique kubwerera kuno kumudzi.

Pakali pano Avant publications mmene imakafika pamalopo inakakumana ndi apolisi akumanga anthu omwe akuganiziridwa kuti anatengapo mbali pa nkhaniyi. Mmene Avant publications imalemba nkhaniyi nkuti galimoto yapolisi yayenda maulendo awiri kudzatuta anthu oganiziridwawo.

www.avantmalawi.com🇲🇼

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *