olemba Dr mwale
Zinali ngati zocheza pomwe patienceNamadingo anapemba khonsolo ya mzinda wa brantyre kuti agwiritse ntchito malo omwe pamafunika kuikidwa chifanifani cha mahatmagand kuti iye ayimepo ndikupempha chithandizo Cha mnyamata otchedwa william kachigamba kuti akathandizidwe ku Zambia pa vuto lake la khansa.
Atapatsidwa chilolezo Namadingo anaima pamalopo masana a lero 25august mpaka madzulo ndicholinga choti apeze ndalama yokwana 3 million.
Mmene anaima pamalopa anthu ena amaona ngati wasowa chochita koma iye anali akudziwa www.avantmalawi.com chomwe akuchita chodabwitsa komanso chotsangalatsa ndi chakuti mmene amatha maola awiri mkuluyi anali atapeza ndalama zoposera 2 million.
Ndipo Namadingo anapitiliza kuima pamalopo osatopa mpaka 6 koloko madzulo ndipo mwachikhulupiliro chake pamene amatsikapo Namadingo anali atakwanilitsa ndalama zokwana 3million zomwe zimatumizidwa ku account yake komanso pa Airtel money zomwe zatsimikizira kuti akachigamba tsopano apita ku Zambia kukalandira thandizo.
Namadingo ali ndi mtima othandiza ndipo kuchita izi oyimbayu sikoyamba, ngati mukukumbukira anathandizapo anthu ena powapezera thandizo ngati lomweri pomaimba nyimbo zake pa mtengo wa 3,000 kwa aliyense yemwe amamuitana, lero ndi uyu wapanga izi.www.avantmalawi.com kunena zoona mulungu amagawa luso ndipo mkuluyi mulungu anamudalitsa ndipo Tipemphe mulungu amudalitse mkuluyi ndipo ku Zambia a William kachigamba akathandizidwe ndikubwerako bwino.
Avant publications ikuyamikira aliyense yemwe watenga mbali kuthandiza kuti zolinga za Namadingo zitheke ndipo ife tikupatsirani zonse zomwe zichitike pa ulendo wa a William kachigamba.
CHAKWERA APULUMUTSA NAMADINGO
Atakhala kwa maola anayi pa malo omwe Namadingo anaima kuti apeze thandizo la a William kachigamba president chakwera anaziwitsidwa za cholinga Cha Namadingo ndipo iye analamula kuti oyimbayu atsike ndipo ndalama yotsalayo amalizitsa ndi iyeyo apa ndipamene Namadingo anatsika pamolopo.
Koma tinene kuti mmene a president analamula izi nkuti mkuluyu atapeza kale ndalama zoposera 3 million
Tsatirani ife pa www.avantmalawi.com