THE MATTER IS IN COURT

Olemba Dr mwale

pempho la chisale likanidwa

bwalo la milandu mdziko muno lakana pempho la yemwe anali wachitetezo wamtsogoleri wakale wa dziko lino, a Norman Chisale loti boma lisawamangenso pa milandu yawo ina yomwe anapalamula.

Poyamba lawyer wa achisale anakagwada ku high court pankhaniyi komwe anamukanira ndipo posakhutitsidwa ndi chigamulocho anakagwadanso ku bwalo lalikulu la supreme komwe atakumana koyamba nkhaniyi anaimitsa kuti azaimve tsiku Lina,

Lero atamaliza kumva mbali zonse judge Lovemore chikopa wagamula kuti pempho la achisale ndilosamveka po nena kuti kugamula kutero ndikulowerera ntchito za apolice zomwe sizifunika kutero.

Izi zikuthandauza kuti achisale atha kumangidwabe pa mlandu ulionse omwe boma lingawapeze nawo.

Pakadali pano a Chisale akadali muchitokosi Cha apolice pa mlandu wokupha a Issa njauju.

Achisale amangidwapo katatu chilowereni boma la Tonse.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *