By Vinjeru Ngwira
Matthias Bonongwe yemwe sabata yapitayi anatuma gulu la chiwembu kuti likalande katundu kwa Bambo Herbert Chimulirenji ku Likuni, akuyenda chothawathawa chifukwa chozemba angongole amene akhala akuwalonjeza zambiri. Pambali pothawathawa apolisi amene akuwafuna pamlandu wokonza chiwembu komanso kusokoneza mtendere, a Matthias Bonongwe anapalamula ngongole zochuluka pogwiritsa ntchito kampani yotchedwa Agri-Zone International Trading (AZIT).
Koma kafukufuku wapeza kuti kampaniyi, imene inali ndi ma office ake mu Area 14 ku Lilongwe inadilizika pamene ochita nawo business achi’Burundi anatulutsa ndalama zawo mu kampaniyi. Mipando, ma kompyuta ndi katundu yense wogwilira ntchito pa kampaniyi anatha ndikugulitsidwa ndinso kulandidwa mokuti Matthias Bonongwe anakakamizika kutseka business pamalowa.
Ngakhale kampaniyi inasiya kuchita malonda aliwonse, Bonongwe akadinditsa ma T-shirt olembapo “AZIT” nkukusa anthu kuwaveka zovalazi pa chipongwe chake cha ku Likuni kwa Bambo Everton Herbert Chimulirenji kuti anthu awone ngati idakalipo.
Tikunena pano Matthias Bonongwe akuthawa magulu awiri: a Police komanso anthu amene anawazembetsera ndalama ndi katundu wawo.