MA INTERVIEW A POLICE ACHITIKANSO

olemba dr mwale

Boma kudzera mwa nduya ya za n’dziko a Richard Chimwendo Banda awuza atola nkhani kuti ndondomeko yolemba ntchito apolice yomwe inachitika miyezi ingapo yapitayo ndi boma la DPP ichitikanso www.avantmalawi.com chifukwa chakuti panali zolakwika zambiri.

Malingana ndi boma la Tonse iwo akuti akufuna pasakhale kukondera pa kachitidwe ka mayeso olowera ku police.
Anthu ambiri omwe anachita nawo mayesowa anali odandaula Malingana ndi ndondomeko yomwe anaika yothamanga ponena kuti anthu ambiri sangakwanitse kuthamanga mozungulira bwalo la zamasewero kokwana ka Khumi pa mphindi khumi ndi zisanu kwa anyamata komanso kasanu kwa mphindi khumi kwa atsikana. Apa zikusonyeza kuti anthu ena amalephera maseyowo kamba ka kuthamanga pomwe akanawapatsa mwayi wa mayeso olankhula komanso olemba akanachita bwino ndikukhala apolice odalilira pomwe ena atha kuchita bwino pothamanga pokha kwinaku ndikumalephera.

Malingana ndi nyumba yofalitsa mawu ya avantpublication inapeza kuti anthu ena amagwa ndikukomoka pothamanga ndipo wina anatayapo moyo kamba ka ndondomekoyi ndipo sitikudziwa kuti mayesowo akazayambiranso anthu azathamanganso kapena mayeso othamangawa awachotsa, Kodi anthu azalemberanso kapena azangotenga omwe anatengedwa kale? Awa ndi mafunso omwe achinyamata ali nawo mdziko muno pomwe omwe anatengedwa kale akuti azaitanidwe omwewo ndipo omwe anasiyidwa akuti azalemberenso. Inuyo maganizo anu alipati?

www.avantmalawi.com

DR MWALE

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *