KUNALINJI MSABATAYI?

Olemba Dr Mwale

Sabata yomwe yangothayi ndi sabata yomwe mwachitika zinthu zingapo zomwe ena mwa ife tinaziphonya koma chifukwa choti AVANT PUBLICATIONS ili pano kukudziwitsani zomwe zinachitika ndipo inu simungaziphonyenso ayi.

ZINA MWA NKHANIZI ZILI MOTERE

Boma lisintha maganizo pa malamulo a covid19

kutsatira kufala kwa kachilombo ka Corona, boma linachiona chanzeru kukhazikitsa malamulo omwe cholinga chake ndi kuteteza anthu kuti asatenge matendawa, mwamalamulo onse omwe anakhazikitsidwa Pali malamulo awiri omwe avuta kuti amalawi awatsate.
Lamulo loti aliyense azivala mask akamayenda ndipo akalephera azipereka 10,000 komanso kuti kumalo opempherera kuzikhala anthu 10 okha.

Katswiri was za Malamuro – Chikosa Sulungwe SC

Izi zitangolengezedwa anthu amipingo anayamba kulankhuka ponena kuti kuti iwo samvera zimenezi chifukwa boma silinawafunse maganizo monga iwo ampingo. Zomwe zinazetsa manong’onong’o mdziko muno. Boma linamvera ndipo anakambirana ndikuthetsa mkanganowu ndipo tsopano malamulo omwe alipo ndi okuti anthu azikumana osaposera 100 mu mmalo opempherera.

Tiyamikire boma chifukwa laonetsa kuti ndi boma lomvera ndipo silinataitse nthawi amalawi posintha maganizo.komanso titengerepo mwayi odzudzula boma popanga ziganizo zomwe sakumaziunikira bwino. Tangoganizani munaletsa anthu kuti azisonkhana okwana 10 ku mmalo opempherera,kumaliro anthu 50 koma pasanathe ndi matsiku atatu kumaliro a Mayi Dinala kunali chinantindi Cha anthu kuphatikizapo president. Kodi munationetsa chisanzo chanji? Ife tikakachulukana kumaliro a kumidzi kwathu mukatimanga? Munasankha pa udindo a modecai msiska ndipo iwo anakana ,izi zikusonyeza kuti munangowasankha osawafunsa maganizo awo. Nduna yoona za zimphunzitso zosiyanasiyana a Timothy mtambo nawo asanasankha owathandizira wawo yemwe anthu anakwiya naye ndipo yekha anatula pansi udindo, tikupempha ziganizo zanu mukamapanga muziyamba mwaziunikira mwakuya.
Nanu a Mpingo mukuti sanakufunseni maganizo anu pa nkhani ya anthu okumana mu church Kodi inuyo munawafunsa a khristu anu maganizo awo? Nanu musamangoyanga’ana chopereka muzatiphetsa, maganizo anuwo mukanaliunikiranso boma kuti litsegule ma school ndi anthu osaposera 100 mu kalasi koma mukulephera ,chakuvutani ndi chopereka osati muzitinamiza ayi.

Nkhani yovala mask amalawi tisaitengere chibwana , boma la DPP linakhazikitsa lock down koma inuyo munachita ma demo dziko lonse, lero boma la Tonse likuti lockdown ayi koma aliyense azingovala mask mukuti alakwanso nde chabwino ndi chiti?

A boma Nanu osamangokamba apa ndalama za covid ndi zambiri zomwe zinabwera lembani ntchito aterala osoke ma mask oti anthu agawiridwe, anthu akumudzi sangakwanitse kugula mask.

CHISALE APEMPHA COURT LISAMUMANGENSO

A Norman Chisale

Ngati malamulo amalora ndipo alore izi nde tinene mosabisa kuti tili ndi malamulo ofooka, achisale apempha boma kuti pa milandu yonse yomwe iye anapalamula boma lisazamumangenso koma azikangoonekera ku court basi ndikumapita kunyuma, iye anapha munthu, anaombera mzimayi, anaba ndalama zaboma ma billion nde court kumatenga nthawi kumamva pempho lakeri? A mabwalo ngati mungalore zomwe iye akufuna nde kumalawi kuno bola zomangana zithe.

A LUTEPO AWAKANIRA PEMPHO LAWO

Cachgate man Lutepo anapempha bwalo kuti amubwenzere ndalama zomwe analipira ku court ngati chikolere zoposa K52 million pomva pempheri bwalo lati uyu asataiyitse nthawi amalawi ndipo anamulamula kuti alipirenso 1 million kwacha.

Oswald Lutepo

ALAMULIDWA KULIPIRA 500,000

Bwalo lamilandu ku brantyre linalamula anyamata atatu achigawo chakumwera omwe anajambula vedeo yomwe amazichemerera kuti iwo amadya ndalama kuti apereke K500,000 aliyense apo bii! akakhale ku ndende miyezi khumi ndi isanu ndi itatu(18) komanso anyamatawa alamulidwa kuti aperekeso 100,000 yokhuza zomwe boma laononga pa mulanduwu.

Langizo: achinyamata osaziputa dala zinazi pa mawa umapusa nazo.

BRAIN BANDA ATENGA MALO A MGEME KALILANI

President wa dziko lino DR Chakwera asankha ma undido osiyanasiyana ku nyumba ya chifumu komwa mwa maundino ena ndi kusankhidwa kwa Brian Banda yemwe tsopano ndi oyankhulira president, iyeyu walowa mmalo mwa MGEME KALILANI yemwe anali oyankhulira Peter mthalika, (amalawi asowa inu pa times ).
A Lucius Banda nawo asankhidwa ngati otsogolera achinyamata ndikuwaphunzitsa malutso osiyana siyana.

Brian Banda

Langizo kwa Brian Banda, osamatinamiza ngati momwe amachitira Mgeme Kalilani.

SUKULU ZITSEKULIDWA KU MAYAMBIRILO A SEPTEMBER

monga ananane mtsogoleri wa dziko lino kuti azikhala ndi program sabata iliyonse youza  amalawi zomwe wachita, msabatayi chakwera analankhulapo za kutsegulidw kwa ma sukulu, iye anati anthu omwe akuona zokhuzana kusekulidwa kwa masukulu akukambiranabe ndipo pano akukonza zoti sukulu zitsekulidwe kumayambiliro a September ndipo ma sukukuonse azatsatire njira zonse zopewera Corona.

Koma ngakhale zili chomwechi makolo Ali ndi nkhawa ndi zinthu ziwiri, ana awo atha kutenga Corona komanso kutsatira kutaya chikhukupiriro chawo ndi ma sukulu a boma makolo ambiri amatumiza ana awo ku ma sukulu a private komwenso fees ndi yokwera kwambiri, pano kwatsala masabata awiri kuti tifike September Kodi makolo akwanitsa kulipira fees?

ZAMASEWERO

champions league yavuta ndipo otenga sakudziwika pomwe mateam akusosolana nthenga , monga munamvera kwa mzanga VINJERU NGWIRA kuti PSG inakwapula Atalanta 1-2 pa home ground ndipo inachita kuchokera kumbuyo kuti igonjetse team Imeneyi, Leipzig nayo inafafantha atletico madri 2-1, Bayern yachita kusambisa chokweza team ya Barcelona ndi zigoli zokwana 2-8 zomwe sizichatikikepo mu mbili ya mateam awiriwa, pomwe timayembekezera kuti Manchester city ndi imene izalimbame ndi Bayern ayi ndithu dzulo Lyon yafafantha man city 1-3 pa khomo. Nako ku South Africa gabadihno mhango waphonya yekhayekha mpata omwe anaupeza pa 78 minutes yekhayekha ndi goalkeeper, izi zapangitsa kuti team ya pirate isewere ma game anayi opanda chigoli.

osewera mu Barcelona adandaula

Nkhani zathu zikulu zikulu ndi zomwezi tionanenso sabata ya mawa.

Share this article

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *